-
Yeremiya 23:21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 “Ine sindinatumize aneneriwo, koma anathamanga.
Ine sindinalankhule nawo, koma analosera.+
-
-
Yeremiya 27:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 ‘Ine sindinawatume,’ akutero Yehova, ‘koma iwo akulosera zabodza mʼdzina langa. Mukawamvera ndidzakubalalitsani ndipo ndidzawononga inuyo limodzi ndi aneneri amene akulosera kwa inu.’”+
-
-
Ezekieli 13:3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Tsoka kwa aneneri opusa, amene akungolosera zamʼmutu mwawo pamene sanaone chilichonse.+
-