Deuteronomo 30:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Yehova Mulungu wanu adzabweza kwawo anthu a mtundu wanu amene anagwidwa nʼkupita kudziko lina,+ ndipo adzakuchitirani chifundo+ nʼkukusonkhanitsaninso pamodzi kuchokera pakati pa anthu onse kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsirani.+ Ezekieli 39:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Ndidzabwezeretsa ana a Yakobo+ omwe anatengedwa kupita kumayiko ena ndipo ndidzachitira chifundo nyumba yonse ya Isiraeli.+ Ndi mphamvu zanga zonse, ndidzateteza dzina langa loyera.*+
3 Yehova Mulungu wanu adzabweza kwawo anthu a mtundu wanu amene anagwidwa nʼkupita kudziko lina,+ ndipo adzakuchitirani chifundo+ nʼkukusonkhanitsaninso pamodzi kuchokera pakati pa anthu onse kumene Yehova Mulungu wanu anakubalalitsirani.+
25 Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Ndidzabwezeretsa ana a Yakobo+ omwe anatengedwa kupita kumayiko ena ndipo ndidzachitira chifundo nyumba yonse ya Isiraeli.+ Ndi mphamvu zanga zonse, ndidzateteza dzina langa loyera.*+