-
Ezekieli 23:4, 5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Wamkulu dzina lake anali Ohola,* wamngʼono anali Oholiba.* Akazi amenewa anakhala anga ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi. Ohola akuimira Samariya+ ndipo Oholiba akuimira Yerusalemu.
5 Ohola anayamba kuchita uhule+ ngakhale kuti anali mkazi wanga. Ankalakalaka kugona ndi amuna amene ankamukonda kwambiri+ omwe ndi Asuri amene ankakhala moyandikana naye.+
-
-
Ezekieli 23:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Choncho ndinamʼpereka mʼmanja mwa anthu amene ankamukonda kwambiri, omwe ndi amuna amʼdziko la Asuri+ amene ankalakalaka kugona naye.
-
-
Hoseya 2:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Imbani mlandu mayi anu. Aimbeni mlandu.
Chifukwa iwowo si mkazi wanga+ ndipo ine si mwamuna wawo.
Mayi anuwo asiye uhule*
Komanso asiye kuchita chigololo.*
-