-
Yesaya 10:24, 25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Choncho Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Anthu anga amene mukukhala mʼZiyoni, musachite mantha chifukwa cha Msuri amene ankakukwapulani ndi chikwapu+ ndiponso kukumenyani ndi ndodo, ngati mmene ankachitira Iguputo.+ 25 Chifukwa pakangodutsa kanthawi kochepa, kudzudzulako kudzatha ndipo mkwiyo wanga udzawayakira, moti adzawonongedwa.+
-