-
1 Mafumu 22:17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Choncho Mikaya anati: “Ndikuona Aisiraeli onse atabalalika mʼmapiri+ ngati nkhosa zopanda mʼbusa. Ndipo Yehova anati: ‘Amenewa alibe mtsogoleri. Aliyense abwerere kunyumba kwake mwamtendere.’”
-
-
Ezekieli 34:5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 Choncho zinamwazikana chifukwa zinalibe mʼbusa+ ndipo zinakhala chakudya cha zilombo zonse zakutchire.
-
-
Ezekieli 34:8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 ‘“Pali ine Mulungu wamoyo,” akutero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, “nkhosa zanga zagwidwa ndipo zakhala chakudya cha zilombo zonse zakutchire chifukwa panalibe mʼbusa ndipo abusa anga sanazifunefune. Koma ankangodzidyetsa okha, osadyetsa nkhosa zanga.”’
-