-
Deuteronomo 15:7, 8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Ngati mmodzi mwa abale anu wasauka pakati panu, mu umodzi mwa mizinda yanu mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, musamamuumire mtima kapena kumuumitsira dzanja lanu.+ 8 Koma muzithandiza mʼbale wanuyo mowolowa manja,+ ndipo mulimonse mmene zingakhalire, muzimukongoza* chilichonse chimene akufuna kapena chimene akusowa.
-
-
Miyambo 21:26Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
26 Tsiku lonse amalakalaka chinachake mwadyera,
Koma munthu wolungama amapereka, saumira chilichonse.+
-