8 “Koma iwe Isiraeli, ndiwe mtumiki wanga,+
Iwe Yakobo, amene ndakusankha,+
Mbadwa ya mnzanga Abulahamu.+
9 Iwe amene ndinakutenga kuchokera kumalekezero a dziko lapansi,+
Ndiponso iwe amene ndinakuitana kuchokera kumadera akutali a dziko lapansi.
Ndinakuuza kuti, ‘Iwe ndiwe mtumiki wanga.+
Ndakusankha ndipo sindinakutaye.+