Salimo
Kwa wotsogolera nyimbo, pa Gititi.* Salimo la Asafu.+
81 Fuulani mosangalala kwa Mulungu amene ndi mphamvu yathu.+
Fuulirani Mulungu wa Yakobo mosangalala chifukwa wapambana.
2 Yambani kuimba nyimbo ndipo tengani maseche,
Zeze womveka mosangalatsa pamodzi ndi choimbira cha zingwe.
3 Pa tsiku limene mwezi watsopano waoneka,+ imbani lipenga la nyanga ya nkhosa,
Pa tsiku limene mwezi wathunthu waoneka, imbani lipenga la nyanga ya nkhosa, limene limaimbidwa pa tsiku la chikondwerero.+
4 Chifukwa limeneli ndi lamulo kwa Isiraeli,
Komanso chigamulo cha Mulungu wa Yakobo.+
5 Mulungu anaika chigamulocho kuti chikhale chikumbutso kwa Yosefe+
Pamene ankapita kukapereka chilango mʼdziko la Iguputo.+
Ndinamva mawu amene sindinathe kuwazindikira akuti:*
6 “Ndinachotsa katundu wolemera paphewa lake.+
Manja ake anamasuka moti sankanyamulanso dengu.
7 Pamene unkakumana ndi mavuto unaitana, ndipo ine ndinakupulumutsa.+
Ndinakuyesa pamadzi a ku Meriba.*+ (Selah)
8 Imvani anthu anga, ndipo ine ndipereka umboni wokutsutsani.
Inu Aisiraeli, zikanakhala bwino ngati mukanandimvera.+
9 Pakati panu sipadzakhala mulungu wachilendo,
Ndipo simudzagwadira mulungu wachilendo.+
10 Ine Yehova, ndine Mulungu wanu,
Amene ndinakutulutsani mʼdziko la Iguputo.+
Tsegulani kwambiri pakamwa panu ndipo ndidzaikamo chakudya.+
11 Koma anthu anga sanamvere mawu anga,
Isiraeli sanafune kundigonjera.+
12 Choncho ndinawasiya kuti apitirize kuchita zofuna za mtima wawo wosamverawo.
13 Zikanakhala bwino ngati anthu anga akanandimvera,+
Zikanakhala bwino ngati Isiraeli akanayenda mʼnjira zanga.+
14 Ndikanagonjetsa adani awo mofulumira,
Ndikanalanga adani awo ndi dzanja langa.+
15 Amene amadana ndi Yehova adzachita mantha pamaso pake,
Ndipo zimene zidzawachitikire* zidzakhalapo mpaka kalekale.