Yobu
9 Yobu anayankha kuti:
2 “Ndikudziwa ndithu kuti zili choncho.
Koma kodi munthu anganene bwanji kuti ndi wosalakwa pamaso pa Mulungu?+
3 Ngati munthu akufuna kutsutsana ndi Mulungu,*+
Munthuyo sangathe kuyankha funso ndi limodzi lomwe pamafunso ake 1,000.
4 Iye ali ndi mtima wanzeru ndiponso mphamvu zambiri.+
Ndani angatsutsane naye koma osavulala?+
5 Iye amasuntha* mapiri popanda aliyense kudziwa.
Amawagubuduza atakwiya.
6 Amagwedeza dziko lapansi nʼkulisuntha pamalo ake,
Moti zipilala zake zimagwedera.+
7 Amalamula dzuwa kuti lisawale
Ndipo amaphimba kuwala kwa nyenyezi.+
8 Iye amatambasula kumwamba yekha,+
Ndipo amayenda pamafunde ataliatali a mʼnyanja.+
9 Anapanga gulu la nyenyezi la Asi, la Kesili ndi la Kima,+
Komanso gulu la nyenyezi za kumʼmwera.
10 Amachita zinthu zazikulu ndi zosatheka kuzifufuza,+
Zinthu zodabwitsa zimene ndi zosatheka kuziwerenga.+
11 Iye amadutsa pafupi ndi ine koma sinditha kumuona,
Amandidutsa koma ine osamuzindikira.
12 Iye akalanda chinthu, ndani angalimbane naye?
Ndani angamufunse kuti, ‘Mukuchita chiyani?’+
14 Nʼchifukwa chake ndikamamuyankha,
Ndiyenera kusankha bwino mawu anga.
15 Ngakhale nditakhala kuti ndikunena zoona, sindingamuyankhe.+
Koma ndingachonderere woweruza wanga kuti andichitire chifundo.
16 Kodi nditamuitana, angandiyankhe?
Sindikukhulupirira kuti angandimvetsere.
17 Chifukwa iye wandivulaza ndi mavuto angati mphepo yamkuntho,
Ndipo wachulukitsa mabala anga popanda chifukwa.+
18 Sakulola kuti ndikokeko mpweya,
Ndipo akungopitiriza kuwonjezera mavuto anga.
19 Pa nkhani yokhala ndi mphamvu, iye ndi wamphamvu kwambiri.+
Pa nkhani yochita zinthu mwachilungamo, iye amanena kuti: ‘Ndi ndani angandiimbe mlandu?’*
20 Ngakhale ndikanapezeka kuti ndine wosalakwa, pakamwa panga pakanandiweruza kuti ndine wolakwa.
Ngakhale nditakhala wokhulupirika,* adzandipezabe ndi mlandu.*
21 Ngakhale nditakhala wokhulupirika,* sindikudziwa zimene zingandichitikire,
Moyo wangawu sindikuufunanso.*
22 Zonsezi mfundo yake ndi imodzi. Nʼchifukwa chake ndikunena kuti,
‘Iye amawononga onse, osalakwa* komanso oipa.’
23 Anthu atafa mwadzidzidzi ndi madzi osefukira,
Iye angaseke anthu osalakwa akuvutika.
Ngati si iyeyo, ndiye ndi ndani?
25 Panopa masiku anga akufulumira kwambiri kuposa munthu wothamanga.+
Iwo akuthawa asanaone zabwino.
26 Amayenda mofulumira ngati ngalawa za bango,
Ngati ziwombankhanga zimene zimambwandira nyama yoti zidye.
27 Ngati nditanena kuti, ‘Ndiiwala kudandaula kwanga,
Ndisintha maonekedwe a nkhope yanga nʼkukhala wosangalala,’
28 Ndingachitebe mantha chifukwa cha zopweteka zanga zonse,+
Ndipo ndikudziwa kuti simungandipeze kuti ndine wosalakwa.
29 Ndingapezekebe kuti ndine wolakwa.*
Ndiye ndivutikirenji pachabe?+
30 Nditati ndisambe mʼmadzi oyera,*
Komanso kusamba mʼmanja ndi sopo,+
31 Inuyo mungandiviike mʼdzenje la matope,
Moti ngakhale zovala zanga zomwe zinganyansidwe nane.
32 Chifukwa iye si munthu ngati ine kuti ndingamuyankhe,
Kapena kuti titengerane kukhoti.+