Salimo
Kwa wotsogolera nyimbo. Aimbe nyimboyi pa Sheminiti.* Nyimbo ya Davide.
12 Ndipulumutseni, inu Yehova, chifukwa anthu okhulupirika atha.
Anthu okhulupirika atheratu pakati pa anthu.
2 Iwo amauzana zinthu zabodza.
Ndi milomo yawo, amayamikira ena mwachiphamaso* komanso kulankhula ndi mtima wachinyengo.*+
3 Yehova adzadula milomo yonse yolankhula zachinyengo
Komanso lilime lolankhula modzikweza.+
4 Iye adzadula anthu amene amanena kuti: “Ndi lilime lathu tidzapambana.
Timagwiritsa ntchito milomo yathu mmene tikufunira.
Ndi ndani angatilamulire?”+
5 Yehova wanena kuti: “Chifukwa chakuti ovutika akuponderezedwa
Chifukwa cha kuusa moyo kwa anthu osauka,+
Ndidzanyamuka nʼkuchitapo kanthu,
Ndidzawapulumutsa kwa anthu amene akuwanyoza.”*
6 Mawu a Yehova ndi oyera.+
Ali ngati siliva woyengedwa mungʼanjo yadothi nthawi zokwanira 7.
7 Inu Yehova mudzawayangʼanira.+
Aliyense wa iwo mudzamuteteza ku mʼbadwo uwu mpaka kalekale.
8 Anthu oipa akungoyendayenda popanda wowaletsa,
Chifukwa chakuti ana a anthu amalimbikitsa anthu kuchita zinthu zoipa.+