Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • 1 Atesalonika 4
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

Zimene Zili Mʼbuku la 1 Atesalonika

      • Anawachenjeza kuti azipewa chiwerewere (1-8)

      • Muzikondana kwambiri kuposa mmene mukuchitira (9-12)

        • “Musamalowerere nkhani za ena” (11)

      • Amene anafa mwa Khristu adzakhala oyambirira kuuka (13-18)

1 Atesalonika 4:1

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Akl 1:10; 1Pe 2:12

1 Atesalonika 4:2

Mawu a M'munsi

  • *

    Kapena kuti, “malamulo.”

1 Atesalonika 4:3

Mawu a M'munsi

  • *

    MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Yoh 17:19; Aef 5:25-27; 2At 2:13; 1Pe 1:15, 16
  • +Aef 5:3

1 Atesalonika 4:4

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Akl 3:5; 2Ti 2:22
  • +Aro 6:19

1 Atesalonika 4:5

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Sl 79:6; Aef 4:17, 19; 1Pe 4:3
  • +1Ak 6:18; Aef 5:5

1 Atesalonika 4:6

Mawu a M'munsi

  • *

    Onani Zakumapeto A5.

1 Atesalonika 4:7

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Ahe 12:14; 1Pe 1:15, 16

1 Atesalonika 4:8

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Ak 6:18, 19
  • +1Yo 3:24

1 Atesalonika 4:9

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Aro 12:10
  • +Yoh 13:34, 35; 1Pe 1:22; 1Yo 4:21

1 Atesalonika 4:11

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +2At 3:11, 12
  • +1Pe 4:15
  • +1Ak 4:11, 12; Aef 4:28; 2At 3:10; 1Ti 5:8

1 Atesalonika 4:12

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Aro 12:17

1 Atesalonika 4:13

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Yoh 11:11; Mac 7:59, 60; 1Ak 15:6
  • +1Ak 15:32

1 Atesalonika 4:14

Mawu a M'munsi

  • *

    Kutanthauza Yesu.

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Aro 14:9; 1Ak 15:3, 4
  • +1Ak 15:22, 23; Afi 3:20, 21; 2At 2:1; Chv 20:4

1 Atesalonika 4:15

Mawu a M'munsi

  • *

    Onani Zakumapeto A5.

1 Atesalonika 4:16

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Yuda 9
  • +1Ak 15:51, 52

1 Atesalonika 4:17

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 1:9
  • +2At 2:1
  • +Yoh 14:3; 17:24; 2Ak 5:8; Afi 1:23; Chv 20:6

Malemba Ena

1 Ates. 4:1Akl 1:10; 1Pe 2:12
1 Ates. 4:3Yoh 17:19; Aef 5:25-27; 2At 2:13; 1Pe 1:15, 16
1 Ates. 4:3Aef 5:3
1 Ates. 4:4Akl 3:5; 2Ti 2:22
1 Ates. 4:4Aro 6:19
1 Ates. 4:5Sl 79:6; Aef 4:17, 19; 1Pe 4:3
1 Ates. 4:51Ak 6:18; Aef 5:5
1 Ates. 4:7Ahe 12:14; 1Pe 1:15, 16
1 Ates. 4:81Ak 6:18, 19
1 Ates. 4:81Yo 3:24
1 Ates. 4:9Aro 12:10
1 Ates. 4:9Yoh 13:34, 35; 1Pe 1:22; 1Yo 4:21
1 Ates. 4:112At 3:11, 12
1 Ates. 4:111Pe 4:15
1 Ates. 4:111Ak 4:11, 12; Aef 4:28; 2At 3:10; 1Ti 5:8
1 Ates. 4:12Aro 12:17
1 Ates. 4:13Yoh 11:11; Mac 7:59, 60; 1Ak 15:6
1 Ates. 4:131Ak 15:32
1 Ates. 4:14Aro 14:9; 1Ak 15:3, 4
1 Ates. 4:141Ak 15:22, 23; Afi 3:20, 21; 2At 2:1; Chv 20:4
1 Ates. 4:16Yuda 9
1 Ates. 4:161Ak 15:51, 52
1 Ates. 4:17Mac 1:9
1 Ates. 4:172At 2:1
1 Ates. 4:17Yoh 14:3; 17:24; 2Ak 5:8; Afi 1:23; Chv 20:6
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
  • 1
  • 2
  • 3
  • 4
  • 5
  • 6
  • 7
  • 8
  • 9
  • 10
  • 11
  • 12
  • 13
  • 14
  • 15
  • 16
  • 17
  • 18
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
1 Atesalonika 4:1-18

Kalata Yoyamba Yopita kwa Atesalonika

4 Pomalizira abale, tinakupatsani malangizo a mmene muyenera kuyendera kuti muzisangalatsa Mulungu+ ndipo mukuchitadi zimenezo. Ndiye tikukupemphani komanso kukuchondererani mʼdzina la Ambuye Yesu kuti mupitirize kuchita zimenezi kuposa mmene mukuchitira. 2 Chifukwa mukudziwa malangizo* amene tinakupatsani mʼdzina la Ambuye Yesu.

3 Mulungu akufuna kuti mukhale oyera+ komanso kuti muzipewa chiwerewere.*+ 4 Aliyense wa inu azidziwa kulamulira thupi lake+ kuti likhale loyera+ komanso lolemekezeka pamaso pa Mulungu. 5 Musakhale ngati anthu a mitundu ina omwe sadziwa Mulungu+ komanso ali ndi chilakolako chosalamulirika cha kugonana+ ndipo sakhutiritsidwa. 6 Pasapezeke aliyense wopweteka mʼbale wake pa nkhani imeneyi nʼkumubweretsera mavuto, chifukwa Yehova* adzapereka chilango kwa munthu aliyense amene akuchita zinthu zimenezi, monga mmene tinakuuzirani kale komanso kukuchenjezani mwamphamvu. 7 Chifukwa Mulungu sanatiitane kuti tizichita makhalidwe odetsa, koma kuti tikhale oyera.+ 8 Choncho munthu amene akunyalanyaza machenjezo amenewa sakunyalanyaza munthu, koma Mulungu+ amene amakupatsani mzimu wake woyera.+

9 Koma zokhudza kukonda abale,+ nʼzosafunika kuti tichite kukulemberani chifukwa inuyo, Mulungu amakuphunzitsani kuti muzikondana.+ 10 Ndipotu mukuchita kale zimenezi kwa abale onse ku Makedoniya konse. Koma tikukulimbikitsani abale kuti mupitirize kuchita zimenezi kuposa mmene mukuchitira. 11 Muziyesetsa kukhala mwamtendere,+ musamalowerere nkhani za ena+ ndipo muzigwira ntchito ndi manja anu+ mogwirizana ndi malangizo amene tinakupatsani. 12 Muzichita zimenezi kuti mukhale ndi makhalidwe amene angachititse kuti anthu akunja azikulemekezani+ ndiponso kuti mukhale osasowa kanthu.

13 Komanso abale, sitikufuna kuti mukhale osadziwa zokhudza amene akugona mu imfa,+ kuti musakhale ndi chisoni chofanana ndi cha anthu amene alibe chiyembekezo.+ 14 Chifukwa ngati timakhulupirira kuti Yesu anafa nʼkuukitsidwa,+ ndiye kuti Mulungu adzaukitsanso amene akugona mu imfa kudzera mwa Yesu,+ kuti akakhale naye* limodzi. 15 Zimene tikukuuzani mogwirizana ndi mawu a Yehova* nʼzakuti, ife amene tipitirize kukhala ndi moyo mpaka pa nthawi ya kukhalapo kwa Ambuye, sitidzakhala patsogolo pa amene akugona mu imfa. 16 Chifukwa Ambuyewo adzatsika kuchoka kumwamba ndi mfuu yolamula. Mawu awo adzamveka kuti ndi a mkulu wa angelo+ ndipo adzanyamula lipenga la Mulungu mʼdzanja lawo. Ndipo amene anafa mwa Khristu adzakhala oyambirira kuuka.+ 17 Pambuyo pake ife amene tidzakhale tidakali ndi moyo, limodzi ndi iwowo, tidzatengedwa kupita mʼmitambo+ kukakumana ndi Ambuye+ mumlengalenga ndipo tizikakhala ndi Ambuye nthawi zonse.+ 18 Choncho pitirizani kulimbikitsana ndi mawu amenewa.

Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • tumizirani
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • zachinsinsi
  • JW.ORG
  • Lowani
tumizirani