Salimo
Nyimbo ya Davide.
23 Yehova ndi Mʼbusa wanga.+
Sindidzasowa kanthu.+
2 Amandigoneka mʼmalo odyetsera ziweto a msipu wambiri.
Amanditsogolera munjira zachilungamo chifukwa cha dzina lake.+
4 Ngakhale ndikuyenda mʼchigwa chamdima wandiweyani,+
Sindikuopa kanthu,+
Chifukwa inu muli ndi ine.+
Chibonga chanu ndi ndodo yanu zikundipangitsa kumva kuti ndine wotetezeka.*
5 Mumandipatsa chakudya patebulo pamaso pa adani anga.+