Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • Chivumbulutso 12
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

Zimene Zili Mʼbuku la Chivumbulutso

      • Mkazi, mwana wamwamuna ndi chinjoka (1-6)

      • Mikayeli anamenyana ndi chinjoka (7-12)

        • Chinjoka chinaponyedwa padziko lapansi (9)

        • Mdyerekezi akudziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa (12)

      • Chinjoka chinazunza mkazi (13-17)

Chivumbulutso 12:1

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Ge 3:15

Chivumbulutso 12:3

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 12:9; 20:2

Chivumbulutso 12:4

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Yob 38:7
  • +Ge 6:2; Yuda 6
  • +Ge 3:15

Chivumbulutso 12:5

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 11:15
  • +Sl 2:9; 110:2; Chv 19:15

Chivumbulutso 12:6

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 12:14

Chivumbulutso 12:7

Mawu a M'munsi

  • *

    Kutanthauza, “Ndi Ndani Angafanane ndi Mulungu.”

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Da 10:13; 12:1; Yuda 9

Chivumbulutso 12:8

Mawu a M'munsi

  • *

    Mabaibulo ena amati, “koma chinagonjetsedwa,” kutanthauza chinjokacho.

Chivumbulutso 12:9

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 12:3; 20:2
  • +Ge 3:1; 2Ak 11:3; Chv 12:14
  • +Mt 4:1; Yoh 8:44; Ahe 2:14; Yak 4:7; 1Pe 5:8
  • +1Mb 21:1; Yob 1:6; Zek 3:2; Mt 4:10; Yoh 13:27; Aro 16:20; 2At 2:9
  • +2Ak 4:4; 11:14; Aef 2:2; 1Yo 5:19
  • +Lu 10:18; Chv 12:13

Chivumbulutso 12:10

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Aro 13:11; Ahe 9:28; 1Pe 1:5
  • +Chv 11:15, 17
  • +Yob 1:9; Zek 3:1

Chivumbulutso 12:11

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +1Yo 2:14
  • +1Pe 1:18, 19
  • +Mac 1:8; 2Ti 1:8; Chv 1:9
  • +Mt 16:25; Lu 14:26; Mac 20:24

Chivumbulutso 12:12

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Yes 57:20; 60:2; Chv 17:15
  • +Mt 24:34; Aro 16:20; 2Ti 3:1; 2Pe 3:3

Chivumbulutso 12:13

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Lu 10:18
  • +Ge 3:15; Chv 12:1

Chivumbulutso 12:14

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Eks 19:4; Yes 40:31
  • +Chv 12:6
  • +Ge 3:1; 2Ak 11:3

Chivumbulutso 12:17

Mawu a M'munsi

  • *

    Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Ge 3:15
  • +Mt 24:9; Mac 1:8; Chv 1:9; 6:9

Malemba Ena

Chiv. 12:1Ge 3:15
Chiv. 12:3Chv 12:9; 20:2
Chiv. 12:4Yob 38:7
Chiv. 12:4Ge 6:2; Yuda 6
Chiv. 12:4Ge 3:15
Chiv. 12:5Chv 11:15
Chiv. 12:5Sl 2:9; 110:2; Chv 19:15
Chiv. 12:6Chv 12:14
Chiv. 12:7Da 10:13; 12:1; Yuda 9
Chiv. 12:9Chv 12:3; 20:2
Chiv. 12:9Ge 3:1; 2Ak 11:3; Chv 12:14
Chiv. 12:9Mt 4:1; Yoh 8:44; Ahe 2:14; Yak 4:7; 1Pe 5:8
Chiv. 12:91Mb 21:1; Yob 1:6; Zek 3:2; Mt 4:10; Yoh 13:27; Aro 16:20; 2At 2:9
Chiv. 12:92Ak 4:4; 11:14; Aef 2:2; 1Yo 5:19
Chiv. 12:9Lu 10:18; Chv 12:13
Chiv. 12:10Aro 13:11; Ahe 9:28; 1Pe 1:5
Chiv. 12:10Chv 11:15, 17
Chiv. 12:10Yob 1:9; Zek 3:1
Chiv. 12:111Yo 2:14
Chiv. 12:111Pe 1:18, 19
Chiv. 12:11Mac 1:8; 2Ti 1:8; Chv 1:9
Chiv. 12:11Mt 16:25; Lu 14:26; Mac 20:24
Chiv. 12:12Yes 57:20; 60:2; Chv 17:15
Chiv. 12:12Mt 24:34; Aro 16:20; 2Ti 3:1; 2Pe 3:3
Chiv. 12:13Lu 10:18
Chiv. 12:13Ge 3:15; Chv 12:1
Chiv. 12:14Eks 19:4; Yes 40:31
Chiv. 12:14Chv 12:6
Chiv. 12:14Ge 3:1; 2Ak 11:3
Chiv. 12:17Ge 3:15
Chiv. 12:17Mt 24:9; Mac 1:8; Chv 1:9; 6:9
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
  • 1
  • 2
  • 3
  • 4
  • 5
  • 6
  • 7
  • 8
  • 9
  • 10
  • 11
  • 12
  • 13
  • 14
  • 15
  • 16
  • 17
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Chivumbulutso 12:1-17

Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira

12 Kenako kumwamba kunaoneka chizindikiro chachikulu. Kunaoneka mkazi+ atavala dzuwa ndipo mwezi unali pansi pa mapazi ake. Kumutu kwake kunali chisoti chachifumu chopangidwa ndi nyenyezi 12. 2 Mkaziyo anali woyembekezera ndipo ankalira chifukwa cha ululu umene ankamva atatsala pangʼono kubereka.

3 Kumwamba kunaoneka chizindikiro chinanso. Ndinaona chinjoka chachikulu chofiira+ chimene chinali ndi mitu 7 ndi nyanga 10 ndipo pamituyo panali zisoti zachifumu 7. 4 Mchira wake unakokolola gawo limodzi mwa magawo atatu a nyenyezi+ zakumwamba nʼkuzigwetsera padziko lapansi.+ Ndipo chinjokacho chinangoima pamaso pa mkazi+ amene anali atatsala pangʼono kubereka uja, kuti akabereka chidye mwana wakeyo.

5 Mkaziyo anabereka mwana wamwamuna,+ mnyamata amene adzakusa mitundu yonse ya anthu ndi ndodo yachitsulo.+ Ndipo mwana wakeyo anatengedwa msangamsanga nʼkupititsidwa kwa Mulungu ndi kumpando wake wachifumu. 6 Koma mkaziyo anathawira kuchipululu, kumene Mulungu anamukonzera malo, kumenenso akadyetsedwe kwa masiku 1,260.+

7 Ndipo kumwamba kunabuka nkhondo: Mikayeli*+ ndi angelo ake anamenyana ndi chinjoka. Chinjokacho ndi angelo ake chinamenya nkhondo, 8 koma sanapambane* ndipo malo awo sanapezekenso kumwamba. 9 Choncho chinjokacho+ chinaponyedwa pansi, njoka yakale ija,+ imene imadziwika kuti Mdyerekezi+ komanso Satana,+ amene akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.+ Iye anaponyedwa padziko lapansi+ ndipo angelo akenso anaponyedwa naye limodzi. 10 Ndinamva mawu ofuula kumwamba akuti:

“Tsopano chipulumutso,+ mphamvu, Ufumu wa Mulungu wathu+ ndi ulamuliro wa Khristu wake zafika, chifukwa woneneza abale athu waponyedwa pansi. Iye amawaneneza masana ndi usiku pamaso pa Mulungu wathu.+ 11 Iwo anamugonjetsa+ chifukwa cha magazi a Mwanawankhosa+ ndiponso chifukwa cha uthenga umene ankalalikira+ ndipo anali okonzeka kufa.+ 12 Pa chifukwa chimenechi, kumwamba kusangalale ndi onse amene amakhala kumeneko! Tsoka dziko lapansi ndi nyanja,+ chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu ndipo ali ndi mkwiyo waukulu chifukwa akudziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa.”+

13 Ndiye chinjoka chija chitaona kuti achigwetsera padziko lapansi,+ chinazunza mkazi+ amene anabereka mwana wamwamuna uja. 14 Koma mkaziyo anapatsidwa mapiko awiri a chiwombankhanga chachikulu+ kuti aulukire kuchipululu, kumalo ake aja, kumene akuyenera kudyetsedwa kwa nthawi imodzi, nthawi ziwiri ndi hafu ya nthawi,+ kutali ndi chinjoka chija.+

15 Kenako chinjokacho chinalavula madzi ngati mtsinje kuchokera mʼkamwa mwake. Chinalavulira mkazi uja kuti amire mumtsinjewo. 16 Koma dziko lapansi linathandiza mkaziyo. Dzikolo linatsegula pakamwa pake nʼkumeza mtsinje umene chinjoka chija chinalavula kuchokera mʼkamwa mwake. 17 Choncho chinjokacho chinakwiya ndi mkazi uja, moti chinapita kukachita nkhondo ndi mbadwa*+ zake zimene zinatsala, zomwe zimasunga malamulo a Mulungu ndipo zili ndi ntchito yochitira umboni za Yesu.+

Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • tumizirani
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • zachinsinsi
  • JW.ORG
  • Lowani
tumizirani