Miyambo
21 Mtima wa mfumu uli ngati mitsinje yamadzi mʼdzanja la Yehova.+
Amaupititsa kulikonse kumene iye akufuna.+
3 Kuchita zinthu zoyenera komanso zachilungamo
Kumasangalatsa kwambiri Yehova kuposa nsembe.+
4 Maso odzikweza komanso mtima wonyada
Zili ngati nyale imene imatsogolera anthu oipa, koma zimenezi ndi tchimo.+
5 Mapulani a munthu wakhama amamuthandiza kuti zinthu zimuyendere bwino,*+
Koma onse amene amachita zinthu mopupuluma amasauka.+
6 Kupeza chuma pogwiritsa ntchito lilime lonama
Kuli ngati nkhungu imene imachoka mofulumira komanso msampha wakupha.*+
7 Zinthu zachiwawa zimene anthu oipa amachita nʼzimene zidzawawononge,+
Chifukwa amakana kuchita zinthu mwachilungamo.
8 Njira ya munthu wochimwa imakhala yokhotakhota,
Koma zochita za munthu wolungama ndi zowongoka.+
9 Ndi bwino kukhala pakona ya denga la nyumba
Kusiyana ndi kukhala mʼnyumba limodzi ndi mkazi wolongolola.*+
11 Munthu wonyoza akapatsidwa chilango, wosadziwa zinthu amakhala wanzeru,
Ndipo munthu wanzeru akaphunzira zinthu zambiri, amadziwa zinthu.*+
12 Mulungu amene ndi wolungama amayangʼana nyumba ya munthu woipa.
Amagwetsa anthu oipa kuti akumane ndi tsoka.+
13 Aliyense amene amatseka khutu lake kuti asamve kudandaula kwa munthu wonyozeka,
Nayenso adzaitana koma sadzayankhidwa.+
14 Mphatso yoperekedwa mwachinsinsi imathetsa mkwiyo,+
Ndipo chiphuphu choperekedwa mwamseri* chimathetsa ukali waukulu.
15 Wolungama amasangalala akamachita chilungamo,+
Koma anthu ochita zoipa amadana ndi chilungamo.
16 Munthu amene wasochera nʼkusiya kuchita zinthu mozindikira
Adzapumula mʼgulu la anthu akufa.+
17 Munthu amene amakonda zosangalatsa adzasauka.+
Amene amakonda vinyo ndi mafuta sadzalemera.
18 Munthu woipa ndi dipo la munthu wolungama,
Ndipo munthu wochita zachinyengo adzatengedwa mʼmalo mwa anthu owongoka mtima.+
19 Ndi bwino kukhala mʼchipululu
Kusiyana ndi kukhala ndi mkazi wolongolola* komanso wosachedwa kukwiya.+
20 Chuma chamtengo wapatali komanso mafuta zimapezeka mʼnyumba ya munthu wanzeru,+
21 Amene akufunafuna chilungamo ndiponso chikondi chokhulupirika
Adzapeza moyo, chilungamo ndi ulemerero.+
22 Munthu wanzeru amagonjetsa* mzinda wa anthu amphamvu,
Ndipo amawononga mpanda wolimba umene amadalira.+
23 Amene amateteza pakamwa pake komanso lilime lake
Amapewa mavuto.+
24 Munthu wochita zinthu modzikuza amene saganizira zotsatira zake ndi amene mumamuti
Ndi munthu wonyada komanso amene amakonda kudzionetsera ndiponso kudzitamandira.+
25 Zinthu zimene munthu waulesi amalakalaka zidzamupha,
Chifukwa manja ake amakana kugwira ntchito.+
26 Tsiku lonse amalakalaka chinachake mwadyera,
Koma munthu wolungama amapereka, saumira chilichonse.+
27 Nsembe ya munthu woipa ndi yonyansa.+
Ndiye kuli bwanji akaipereka ndi zolinga zoipa!*
28 Mboni yonena mabodza idzawonongedwa,+
Koma munthu amene amamvetsera adzapereka umboni wa zinthu zimene anamva ndipo zidzamuyendera bwino.*
30 Palibe nzeru kapena kuzindikira, kapena malangizo amene angalepheretse zimene Yehova amafuna.+