Yesaya
57 Wolungama wawonongedwa,
Koma palibe amene zikumukhudza.
2 Iye amalowa mumtendere.
Onse amene amayenda mowongoka amapita kukapuma mʼmanda.*
3 “Koma inu bwerani pafupi,
Inu ana a mayi wamatsenga,
Inu ana a munthu wachigololo ndi hule:
4 Kodi mukumuseka ndani?
Kodi mukuyasamulira ndani pakamwa panu ndi kumutulutsira lilime?
Kodi inu si ana a machimo,
Ana a chinyengo,+
5 Amene mukukhala ndi chilakolako champhamvu chogonana pakati pa mitengo ikuluikulu,+
Pansi pa mtengo uliwonse wa masamba ambiri?+
Kodi si inu amene mumapha ana mʼzigwa,*+
Pakati pa matanthwe?
6 Gawo lako lili pamodzi ndi miyala yosalala yamʼchigwa.*+
Inde, gawo lako ndi limeneli.
Ndipo umapereka nsembe zachakumwa, ndiponso mphatso kwa zinthu zimenezi.+
Kodi ine ndikhutire* ndi zinthu zimenezi?
7 Bedi lako unaliika pamwamba pa phiri lalitali ndi lokwezeka.+
Ndipo unapita kumeneko kukapereka nsembe.+
8 Unaika chizindikiro chachikumbutso chako kuseri kwa chitseko ndi kuseri kwa felemu.
Iwe unandisiya ndipo unavula.
Unakwera mtunda nʼkukulitsa bedi lako.
Ndipo unachita nawo pangano.
9 Iwe unatsetserekera kwa Meleki* utatenga mafuta,
Ndiponso utatenga mafuta ochuluka onunkhira.
Unatumiza nthumwi zako kutali kwambiri,
Moti mpaka unatsikira mʼManda.*
10 Watopa chifukwa chotsatira njira zako zambiri,
Koma sunanene kuti, ‘Nʼzopanda phindu!’
Unapeza mphamvu zina.
Nʼchifukwa chake sunafooke.*
11 Kodi unkaopa komanso kuchita mantha ndi ndani
Kuti uyambe kunama?+
Ine sunandikumbukire.+
Palibe chimene unaganizira mumtima mwako.+
Kodi si paja ine ndinakhala chete ndipo sindinachitepo kanthu pa zochita zako?+
Choncho iweyo sunkandiopa.
13 Ukamafuula popempha thandizo,
Mafano amene unasonkhanitsa sadzakupulumutsa.+
Mphepo idzaulutsa mafano onsewo
Ndipo mpweya udzawakankhira kutali,
Koma munthu amene amathawira kwa ine adzalandira dziko
Ndipo adzatenga phiri langa loyera kukhala lake.+
14 Ndiyeno wina adzanena kuti, ‘Konzani msewu! Konzani msewu! Konzani njira!+
Chotsani chopinga chilichonse panjira ya anthu anga.’”
15 Chifukwa Wapamwamba ndi Wokwezeka,
Amene adzakhalepo mpaka kalekale+ ndiponso dzina lake ndi loyera,+ wanena kuti:
“Ine ndimakhala pamalo apamwamba komanso oyera,+
Koma ndimakhalanso ndi anthu opsinjika ndiponso amene ali ndi mtima wodzichepetsa,
Kuti nditsitsimutse mtima wa anthu onyozeka
Ndiponso kuti nditsitsimutse mtima wa anthu opsinjika.+
16 Chifukwa ine sindidzatsutsana nawo mpaka kalekale
Kapena kukhala wokwiya nthawi zonse.+
Popeza mzimu wa munthu ukhoza kufooka chifukwa cha ine,+
Ngakhale zinthu zopuma zimene ine ndinapanga.
17 Ine ndinakwiya chifukwa cha machimo amene ankachita pofuna kupeza phindu mwachinyengo,+
Choncho ndinamulanga, ndinabisa nkhope yanga ndipo ndinakwiya.
Koma iye anapitiriza kuyenda ngati wopanduka,+ ankangotsatira zofuna za mtima wake.
18 Ine ndaona njira zake,
Koma ndidzamuchiritsa+ nʼkumutsogolera,+
Ndipo ndidzayambiranso kumutonthoza,+ iyeyo ndi anthu ake amene akulira.”+
19 “Ndikulenga chipatso cha milomo.
Mtendere wosatha udzaperekedwa kwa amene ali kutali
Ndiponso kwa amene ali pafupi+ ndipo ndidzamʼchiritsa,” akutero Yehova.
20 “Koma anthu oipa ali ngati nyanja imene ikuchita mafunde, imene singathe kukhala bata,
Ndipo madzi ake akuvundula zomera zamʼnyanjamo ndiponso matope.
21 Oipa alibe mtendere,”+ akutero Mulungu wanga.