Miyambo
20 Munthu amene amamwa vinyo wambiri amayamba kunyoza+ ndipo amene amamwa mowa wambiri amachita zosokoneza.+
Aliyense amene amasochera ndi zinthu zimenezi alibe nzeru.+
2 Kuopsa kwa mfumu kuli ngati kubangula kwa mkango wamphamvu.+
Aliyense woputa mkwiyo wake akuika moyo wake pangozi.+
4 Waulesi salima nthawi yozizira,
Choncho iye azidzapemphapempha nthawi yokolola chifukwa adzakhala alibe kanthu.*+
5 Maganizo amumtima* mwa munthu ali ngati madzi akuya,
Koma munthu wozindikira ndi amene amawatunga.
6 Anthu ambiri amanena kuti ali ndi chikondi chokhulupirika,
Koma ndi ndani amene angapeze munthu wokhulupirika?
7 Munthu wolungama amachita zinthu mokhulupirika.+
Ana ake ndi osangalala.+
12 Khutu lakumva ndiponso diso loona,
Zonsezi anazipanga ndi Yehova.+
13 Usamakonde tulo chifukwa ungasauke.+
Tsegula maso ako ndipo udzakhala ndi chakudya chambiri.+
14 Wogula amanena kuti, “chinthu ichi si chabwino, si chabwino chimenechi!”
Kenako amachoka ndipo amayamba kudzitama.+
15 Pali golide komanso miyala yambiri yamtengo wapatali ya korali,*
Koma milomo yodziwa zinthu ndi yamtengo wapatali.+
16 Ngati munthu walonjeza kuti akhala chikole kwa mlendo, umulande chovala chake.+
Komanso umulande chikole ngati walonjeza zimenezi kwa mkazi wachilendo.+
17 Chakudya chimene munthu wachipeza mwachinyengo chimamukomera,
Koma pambuyo pake mʼkamwa mwake mumadzaza miyala.+
18 Anthu akakambirana zolinga zawo zimakwaniritsidwa,*+
Ndipo uzitsatira malangizo anzeru pomenya nkhondo yako.+
19 Wonenera anzake zoipa amayendayenda nʼkumaulula zinsinsi.+
Usamagwirizane ndi munthu amene amakonda kunena miseche.*
20 Aliyense amene amatemberera bambo ake komanso mayi ake,
Nyale yake idzazimitsidwa kukagwa mdima.+
21 Munthu akapeza cholowa mwadyera,
Pamapeto pake Mulungu sadzamudalitsa.+
22 Usanene kuti: “Ndidzabwezera choipa.”+
Yembekezera Yehova+ ndipo iye adzakupulumutsa.+
23 Miyala yachinyengo* yoyezera ndi yonyansa kwa Yehova,
Ndipo masikelo achinyengo si abwino.
24 Yehova ndi amene amatsogolera mapazi a munthu.+
Ndiye munthu payekha angadziwe bwanji njira yoyenera kuyenda?
25 Umakhala msampha munthu akathamangira kufuula kuti, “Nʼzoyera!”+
Koma pambuyo polonjeza nʼkuyamba kuganiziranso bwino zimene walonjezazo.+
27 Mpweya wa munthu ndi nyale ya Yehova.
Imafufuza zinthu zamkati mwa mtima wake.
28 Kukhulupirika komanso chikondi chokhulupirika zimateteza mfumu.+
Mfumuyo ikamasonyeza chikondi chokhulupirika, mpando wake wachifumu umakhazikika.+
30 Mabala obwera chifukwa chopatsidwa chilango amachotsa zoipa,+
Ndipo zikwapu zimayeretsa mtima wa munthu.