Miyambo
25 Miyambi ina ya Solomo+ imene atumiki a Hezekiya+ mfumu ya Yuda anakopera ndi iyi:
2 Kusunga chinsinsi ndi ulemerero wa Mulungu,+
Ndipo ulemerero wa mafumu ndi kufufuza bwino nkhani.
3 Nʼzosatheka kufufuza kutalika kwa kumwamba komanso kuzama kwa dziko lapansi,
Nʼchimodzimodzinso mitima ya mafumu.
4 Yengani siliva nʼkuchotsa zonse zosafunika,
Ndipo yense adzatuluka woyengeka bwino.+
5 Chotsani woipa pamaso pa mfumu,
Ndipo mpando wake wachifumu udzakhazikika chifukwa cha chilungamo.+
6 Usadzilemekeze wekha pamaso pa mfumu,+
Ndipo usakhale pakati pa anthu olemekezeka,+
7 Chifukwa ndi bwino kuti mfumuyo ikuuze kuti, “Bwera udzakhale apa,”
Kusiyana nʼkuti ikuchititse manyazi pamaso pa munthu wolemekezeka.+
8 Usamafulumire kupititsa mlandu kukhoti,
Chifukwa udzachita chiyani mnzako akadzapereka umboni wosonyeza kuti iweyo ndi wolakwa?+
9 Thetsa nkhaniyo pokambirana ndi mnzakoyo,+
Koma usaulule nkhani zachinsinsi zimene unauzidwa,*+
10 Kuti amene akumvetsera asakuchititse manyazi
Komanso kuti usafalitse nkhani yoipa* imene sungathe kuithetsa kuti isapitirize kufalikira.
11 Mawu olankhulidwa pa nthawi yoyenera+
Ali ngati zipatso za maapozi agolide mʼmbale zasiliva.
12 Munthu wanzeru akamadzudzula munthu wa khutu lomvetsera+
Amakhala ngati ndolo yagolide ndiponso ngati chokongoletsera chagolide woyenga bwino.
13 Nthumwi yokhulupirika kwa anthu amene aituma
Ili ngati kuzizira kwa sinowo* pa tsiku lokolola,
Chifukwa imatsitsimula moyo wa abwana ake.+
14 Munthu wodzitama kuti apereka mphatso koma nʼkulephera kupereka,+
Ali ngati mitambo komanso mphepo yosabweretsa mvula.
15 Chifukwa cha kuleza mtima munthu angathe kunyengerera munthu waudindo,
16 Ukapeza uchi udye umene ungakukwane,
Chifukwa ukadya wambiri ungathe kuusanza.+
17 Phazi lako lisamapitepite kunyumba kwa mnzako,
Kuti angatope nawe nʼkuyamba kudana nawe.
18 Munthu wopereka umboni wabodza pa mlandu wa mnzake+
Ali ngati chibonga chakunkhondo, lupanga, komanso muvi wakuthwa.
19 Kukhulupirira munthu wosadalirika* pa nthawi yamavuto
Kuli ngati dzino lothyoka komanso phazi lotsimphina.
20 Amene amaimbira nyimbo munthu amene ali ndi chisoni mumtima mwake+
Ali ngati munthu amene amavula chovala pa tsiku lozizira,
Komanso ngati viniga* amene wathiridwa musoda
21 Ngati mdani wako* ali ndi njala, umʼpatse chakudya.
Ngati ali ndi ludzu, umʼpatse madzi akumwa,+
22 Ukachita zimenezi ndiye kuti ukumuunjikira makala amoto pamutu pake,*+
Ndipo Yehova adzakupatsa mphoto.
23 Mphepo yakumpoto imabweretsa mvula yambiri
Ndipo lilime lonena miseche limachititsa kuti anthu akhale ndi nkhope zolusa.+
24 Ndi bwino kukhala pakona ya denga la nyumba
Kusiyana ndi kukhala mʼnyumba limodzi ndi mkazi wolongolola.*+
25 Nkhani yabwino yochokera kudziko lakutali+
Ili ngati madzi ozizira kwa munthu wotopa.
26 Munthu wolungama amene amagonja* nʼkuchita zofuna za munthu woipa
Amakhala ngati kasupe wamatope komanso chitsime chimene chawonongedwa.
28 Munthu wosaugwira mtima+
Ali ngati mzinda umene mpanda wake wagumulidwa.