Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • Chivumbulutso 7
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

Zimene Zili Mʼbuku la Chivumbulutso

      • Angelo 4 anagwira mphepo kuti zisawononge (1-3)

      • Anthu okwana 144,000 anaikidwa chidindo (4-8)

      • Khamu lalikulu limene lavala mikanjo yoyera (9-17)

Chivumbulutso 7:2

Mawu a M'munsi

  • *

    Kapena kuti, “kuchokera kumʼmawa.”

Chivumbulutso 7:3

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +2Ak 1:22; Aef 1:13; 4:30
  • +Chv 9:4

Chivumbulutso 7:4

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 14:1, 3
  • +Aro 2:29; 9:6; Aga 6:16; Chv 21:12

Chivumbulutso 7:6

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Ge 41:51

Chivumbulutso 7:9

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Yes 2:2; Chv 15:4
  • +Chv 7:14
  • +Le 23:40; Yoh 12:13

Chivumbulutso 7:10

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 4:2, 3
  • +Mac 4:12; Chv 5:6

Chivumbulutso 7:11

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 4:4; 11:16

Chivumbulutso 7:12

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 4:11

Chivumbulutso 7:13

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 7:9

Chivumbulutso 7:14

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mt 24:21; Mko 13:19
  • +Yoh 1:29; Ahe 9:14; 1Yo 1:7; Chv 1:5

Chivumbulutso 7:15

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 4:2
  • +Sl 15:1; Chv 21:3

Chivumbulutso 7:16

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Sl 121:6; Yes 49:10

Chivumbulutso 7:17

Mawu a M'munsi

  • *

    Mʼchilankhulo choyambirira, “ali pakati.”

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 5:6
  • +Yoh 10:11
  • +Chv 22:1
  • +Yes 25:8; Chv 21:4

Malemba Ena

Chiv. 7:32Ak 1:22; Aef 1:13; 4:30
Chiv. 7:3Chv 9:4
Chiv. 7:4Chv 14:1, 3
Chiv. 7:4Aro 2:29; 9:6; Aga 6:16; Chv 21:12
Chiv. 7:6Ge 41:51
Chiv. 7:9Yes 2:2; Chv 15:4
Chiv. 7:9Chv 7:14
Chiv. 7:9Le 23:40; Yoh 12:13
Chiv. 7:10Chv 4:2, 3
Chiv. 7:10Mac 4:12; Chv 5:6
Chiv. 7:11Chv 4:4; 11:16
Chiv. 7:12Chv 4:11
Chiv. 7:13Chv 7:9
Chiv. 7:14Mt 24:21; Mko 13:19
Chiv. 7:14Yoh 1:29; Ahe 9:14; 1Yo 1:7; Chv 1:5
Chiv. 7:15Chv 4:2
Chiv. 7:15Sl 15:1; Chv 21:3
Chiv. 7:16Sl 121:6; Yes 49:10
Chiv. 7:17Chv 5:6
Chiv. 7:17Yoh 10:11
Chiv. 7:17Chv 22:1
Chiv. 7:17Yes 25:8; Chv 21:4
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
  • 1
  • 2
  • 3
  • 4
  • 5
  • 6
  • 7
  • 8
  • 9
  • 10
  • 11
  • 12
  • 13
  • 14
  • 15
  • 16
  • 17
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Chivumbulutso 7:1-17

Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira

7 Zimenezi zitatha, ndinaona angelo 4 ataimirira mʼmakona 4 a dziko lapansi. Iwo anali atagwira mwamphamvu mphepo 4 za dziko lapansi, kuti mphepo iliyonse isawombe padziko lapansi, panyanja kapena pamtengo uliwonse. 2 Ndinaonanso mngelo wina akukwera kuchokera kotulukira dzuwa,* ali ndi chidindo cha Mulungu wamoyo. Iye anafuula mokweza mawu kwa angelo 4, amene anapatsidwa mphamvu zowononga dziko lapansi ndi nyanja aja, 3 kuti: “Musawononge dziko lapansi, kapena nyanja, kapena mitengo, mpaka titadinda chidindo+ pazipumi za akapolo a Mulungu wathu.”+

4 Ndiyeno ndinamva chiwerengero cha amene anadindidwa chidindo. Anthu okwana 144,000,+ ochokera mʼfuko lililonse la ana a Isiraeli, anadindidwa chidindo:+

5 Mu fuko la Yuda, anadindamo anthu 12,000.

Mu fuko la Rubeni, 12,000.

Mu fuko la Gadi, 12,000.

6 Mu fuko la Aseri, 12,000.

Mu fuko la Nafitali, 12,000.

Mu fuko la Manase,+ 12,000.

7 Mu fuko la Simiyoni, 12,000.

Mu fuko la Levi, 12,000.

Mu fuko la Isakara, 12,000.

8 Mu fuko la Zebuloni, 12,000.

Mu fuko la Yosefe, 12,000.

Ndipo mu fuko la Benjamini, anadindamo anthu 12,000.

9 Zimenezi zitatha, nditayangʼana ndinaona khamu lalikulu la anthu, amene palibe munthu aliyense amene anatha kuwawerenga, ochokera mʼdziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse ndi chilankhulo chilichonse.+ Iwo anali ataimirira pamaso pa mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atavala mikanjo yoyera+ ndiponso atanyamula nthambi za kanjedza mʼmanja mwawo.+ 10 Iwo anapitiriza kufuula ndi mawu okweza akuti: “Chipulumutso chathu chachokera kwa Mulungu wathu, amene wakhala pampando wachifumu,+ ndi kwa Mwanawankhosa.”+

11 Angelo onse anali ataima kuzungulira mpando wachifumu, akulu+ komanso angelo 4 aja. Ndipo onse anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi, pamaso pa mpando wachifumuwo ndi kulambira Mulungu. 12 Iwo ankanena kuti: “Ame! Mulungu wathu ndi amene ali ndi nzeru, mphamvu komanso nyonga ndipo ndi amene akuyenera kutamandidwa, kupatsidwa ulemerero ndi ulemu komanso kuyamikiridwa mpaka kalekale.+ Ame.”

13 Ndiyeno mmodzi wa akulu aja anandifunsa kuti: “Kodi amene avala mikanjo yoyerawa+ ndi ndani ndipo achokera kuti?” 14 Nthawi yomweyo, ndinamuyankha kuti: “Mbuyanga, mukudziwa ndinu.” Ndipo iye anandiuza kuti: “Amenewa ndi amene atuluka mʼchisautso chachikulu+ ndipo achapa mikanjo yawo nʼkuiyeretsa mʼmagazi a Mwanawankhosa.+ 15 Nʼchifukwa chake ali pamaso pa mpando wachifumu wa Mulungu. Iwo akumuchitira utumiki wopatulika usana ndi usiku mʼkachisi wake, ndipo Amene wakhala pampando wachifumuyo+ adzawaphimba ndi tenti yake kuti awateteze.+ 16 Iwo sadzamvanso njala kapena ludzu. Dzuwa kapena kutentha kulikonse sikudzawawotcha,+ 17 chifukwa Mwanawankhosa,+ amene ali pambali* pa mpando wachifumu, adzawaweta+ nʼkuwatsogolera ku akasupe a madzi a moyo.+ Ndipo Mulungu adzapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo.”+

Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • tumizirani
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • zachinsinsi
  • JW.ORG
  • Lowani
tumizirani