Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • Chivumbulutso 20
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

Zimene Zili Mʼbuku la Chivumbulutso

      • Satana adzamangidwa kwa zaka 1,000 (1-3)

      • Amene adzalamulire ndi Khristu kwa zaka 1,000 (4-6)

      • Satana adzamasulidwa, kenako adzawonongedwa (7-10)

      • Akufa adzaweruzidwa pamaso pa mpando wachifumu woyera (11-15)

Chivumbulutso 20:1

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 9:1

Chivumbulutso 20:2

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 12:3
  • +Ge 3:1
  • +Yoh 8:44
  • +Zek 3:1; Chv 12:9

Chivumbulutso 20:3

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 9:11
  • +Chv 20:7

Chivumbulutso 20:4

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 13:15-17
  • +Mt 19:28; Lu 22:28-30; 2Ti 2:12; Chv 1:6

Chivumbulutso 20:5

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 24:15
  • +1Ak 15:23, 52; Afi 3:10, 11; 1At 4:16

Chivumbulutso 20:6

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 14:13
  • +Chv 2:11; 20:14
  • +1Ak 15:54
  • +1Pe 2:9
  • +Chv 1:6; 5:9, 10

Chivumbulutso 20:9

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +2Mf 1:10

Chivumbulutso 20:10

Mawu a M'munsi

  • *

    Kapena kuti, “iwo adzaikidwa mʼndende.”

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 13:1
  • +Chv 19:20

Chivumbulutso 20:11

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 4:2, 3
  • +2Pe 3:7

Chivumbulutso 20:12

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Eks 32:33; Sl 69:28; Da 12:1
  • +Yoh 5:28, 29

Chivumbulutso 20:13

Mawu a M'munsi

  • *

    Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Mac 10:42

Chivumbulutso 20:14

Mawu a M'munsi

  • *

    Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Yes 25:8; 1Ak 15:26
  • +Mt 5:22; 18:9; Chv 21:8
  • +Chv 2:11; 20:6

Chivumbulutso 20:15

Malifalensi Opezeka Pakati pa Tsamba

  • +Chv 17:8
  • +Miy 10:7

Malemba Ena

Chiv. 20:1Chv 9:1
Chiv. 20:2Chv 12:3
Chiv. 20:2Ge 3:1
Chiv. 20:2Yoh 8:44
Chiv. 20:2Zek 3:1; Chv 12:9
Chiv. 20:3Chv 9:11
Chiv. 20:3Chv 20:7
Chiv. 20:4Chv 13:15-17
Chiv. 20:4Mt 19:28; Lu 22:28-30; 2Ti 2:12; Chv 1:6
Chiv. 20:5Mac 24:15
Chiv. 20:51Ak 15:23, 52; Afi 3:10, 11; 1At 4:16
Chiv. 20:6Chv 14:13
Chiv. 20:6Chv 2:11; 20:14
Chiv. 20:61Ak 15:54
Chiv. 20:61Pe 2:9
Chiv. 20:6Chv 1:6; 5:9, 10
Chiv. 20:92Mf 1:10
Chiv. 20:10Chv 13:1
Chiv. 20:10Chv 19:20
Chiv. 20:11Chv 4:2, 3
Chiv. 20:112Pe 3:7
Chiv. 20:12Eks 32:33; Sl 69:28; Da 12:1
Chiv. 20:12Yoh 5:28, 29
Chiv. 20:13Mac 10:42
Chiv. 20:14Yes 25:8; 1Ak 15:26
Chiv. 20:14Mt 5:22; 18:9; Chv 21:8
Chiv. 20:14Chv 2:11; 20:6
Chiv. 20:15Chv 17:8
Chiv. 20:15Miy 10:7
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
  • 1
  • 2
  • 3
  • 4
  • 5
  • 6
  • 7
  • 8
  • 9
  • 10
  • 11
  • 12
  • 13
  • 14
  • 15
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Chivumbulutso 20:1-15

Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira

20 Ndipo ndinaona mngelo akutsika kuchokera kumwamba ali ndi kiyi wa phompho+ ndi tcheni chachikulu mʼdzanja lake. 2 Kenako anagwira chinjoka,+ njoka yakale ija,+ amene ndi Mdyerekezi+ ndiponso Satana,+ nʼkumumanga kwa zaka 1,000. 3 Ndipo anamuponyera mʼphompho+ nʼkutseka pakhomo la phompholo kenako anaikapo chidindo kuti asasocheretsenso mitundu ya anthu mpaka zaka 1,000 zitatha. Pambuyo pake, adzamasulidwa kanthawi kochepa.+

4 Kenako ndinaona mipando yachifumu ndipo amene anakhala pamipandoyo anapatsidwa mphamvu zoweruza. Ndinaona miyoyo ya anthu amene anaphedwa chifukwa chochitira umboni za Yesu komanso chifukwa cholankhula za Mulungu. Inde, ndinaona miyoyo ya anthu amene sanalambire chilombo kapena chifaniziro chake ndipo sanalandire chizindikiro pazipumi zawo ndi padzanja lawo.+ Iwo anakhalanso ndi moyo ndipo analamulira monga mafumu limodzi ndi Khristu+ kwa zaka 1,000. 5 (Akufa enawo+ sanakhalenso ndi moyo mpaka zaka 1,000 zitatha.) Uku ndi kuuka koyamba kwa akufa.+ 6 Wosangalala komanso woyera ndi aliyense amene akuuka nawo pa kuuka koyamba.+ Imfa yachiwiri+ ilibe ulamuliro pa amenewa.+ Koma adzakhala ansembe+ a Mulungu ndi a Khristu, ndipo adzalamulira monga mafumu limodzi ndi Khristu zaka 1,000.+

7 Ndiye zaka 1,000 zimenezi zikadzangotha, Satana adzamasulidwa mʼndende yake, 8 ndipo adzatuluka kukasocheretsa mitundu ya anthu kumakona onse 4 a dziko lapansi. Mitunduyo ndi Gogi komanso Magogi ndipo adzaisonkhanitsa pamodzi kuti amenye nkhondo. Iwo ndi ochuluka ngati mchenga wakunyanja. 9 Iwo adzafalikira padziko lonse lapansi ndipo adzazungulira msasa wa oyera komanso mzinda wokondedwa. Koma moto udzatsika kuchokera kumwamba nʼkuwapsereza.+ 10 Mdyerekezi, amene ankawasocheretsa, adzaponyedwa mʼnyanja yamoto ndi sulufule, mmene muli kale chilombo+ ndi mneneri wabodza uja.+ Ndipo iwo adzazunzidwa masana ndi usiku* mpaka kalekale.

11 Kenako ndinaona mpando wachifumu waukulu woyera komanso Mulungu atakhala pampandowo.+ Dziko lapansi ndi kumwamba zinathawa pamaso pake+ ndipo sizinapezekenso. 12 Ndiye ndinaona akufa, olemekezeka ndi onyozeka, ataimirira pamaso pa mpando wachifumuwo, ndipo mipukutu inatambasulidwa. Koma panali mpukutu wina umene unatambasulidwa, womwe ndi mpukutu wa moyo.+ Akufa anaweruzidwa potengera zimene zinalembedwa mʼmipukutuyo, mogwirizana ndi ntchito zawo.+ 13 Nyanja inapereka akufa amene anali mmenemo. Imfa komanso Manda* zinapereka akufa amene anali mmenemo. Aliyense payekha anaweruzidwa mogwirizana ndi ntchito zake.+ 14 Ndipo imfa ndi Manda* zinaponyedwa mʼnyanja yamoto.+ Nyanja yamoto+ imeneyi ikuimira imfa yachiwiri.+ 15 Komanso, aliyense amene dzina lake silinalembedwe mʼbuku la moyo+ anaponyedwa mʼnyanja yamoto.+

Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • tumizirani
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • zachinsinsi
  • JW.ORG
  • Lowani
tumizirani