Salimo
147 Tamandani Ya!*
Kuimbira Mulungu wathu nyimbo zomutamanda nʼkwabwino,
Kumutamanda nʼkosangalatsa komanso koyenera.+
3 Iye amachiritsa anthu osweka mtima,
Ndipo amamanga mabala awo.
4 Amadziwa chiwerengero cha nyenyezi zonse,
Ndipo iliyonse amaitchula dzina lake.+
6 Yehova amakweza anthu ofatsa,+
Koma anthu oipa amawagwetsera pansi.
7 Imbirani Yehova nyimbo moyamikira.
Imbirani Mulungu wathu nyimbo zomutamanda pogwiritsa ntchito zeze.
8 Imbirani amene amaphimba mapiri ndi mitambo,
Amene amapereka mvula padziko lapansi,+
Amenenso amameretsa udzu+ mʼmapiri.
11 Yehova amasangalala ndi anthu amene amamuopa,+
Amene amayembekezera chikondi chake chokhulupirika.+
12 Lemekeza Yehova, iwe Yerusalemu.
Tamanda Mulungu wako, iwe Ziyoni.
13 Amachititsa kuti mipiringidzo ya mageti ako ikhale yolimba.
Ndipo amadalitsa ana ako.
15 Amapereka lamulo lake padziko lapansi.
Mawu ake amathamanga mofulumira kwambiri.
17 Amaponya matalala ake ngati nyenyeswa za chakudya.+
Ndi ndani angapirire kuzizira kwake?+
18 Amatumiza mawu ake ndipo matalalawo amasungunuka.
Amachititsa mphepo yake kuwomba,+ ndipo madzi amayenda.
19 Yakobo amamuuza mawu ake,
Ndipo Isiraeli amamuuza malangizo ake komanso zigamulo zake.+
20 Sanachite zimenezi ndi mtundu wina uliwonse,+
Ndipo mitundu inayo sikudziwa zigamulo zake.