Salimo
Salimo la Davide, pa nthawi imene anachita zinthu ngati wamisala+ pamaso pa Abimeleki, moti anamuthamangitsa ndipo Davideyo anathawa.
א [Aleph]
34 Ndidzatamanda Yehova nthawi zonse.
Sindidzasiya kumutamanda ndi pakamwa panga.
ב [Beth]
ג [Gimel]
3 Lemekezani Yehova pamodzi ndi ine,+
Tiyeni tonse tikweze dzina lake.
ד [Daleth]
4 Ndinapemphera kwa Yehova ndipo iye anandiyankha.+
Anandipulumutsa ku zinthu zonse zimene zimandichititsa mantha.+
ה [He]
5 Amene anamukhulupirira anasangalala,
Ndipo nkhope zawo sizinachite manyazi.
ז [Zayin]
6 Munthu wonyozekayu anaitana ndipo Yehova anamva.
Anamupulumutsa ku mavuto ake onse.+
ח [Heth]
7 Mngelo wa Yehova amamanga msasa kuzungulira anthu onse amene amaopa Mulungu,+
Ndipo amawapulumutsa.+
ט [Teth]
8 Talawani ndipo muona kuti Yehova ndi wabwino.+
Wosangalala ndi munthu amene amathawira kwa iye.
י [Yod]
9 Opani Yehova, inu oyera ake onse,
Chifukwa onse amene amamuopa sasowa kanthu.+
כ [Kaph]
10 Ngakhale mikango yamphamvu* ingakhale ndi njala chifukwa chosowa chakudya.
Koma anthu amene akufunafuna Yehova sadzasowa chilichonse chabwino.+
ל [Lamed]
11 Bwerani kuno ana anga, ndimvetsereni.
Ndikuphunzitsani kuopa Yehova.+
מ [Mem]
12 Kodi ndi ndani pakati panu amene amakonda moyo,
Ndipo angakonde atakhala ndi moyo wabwino kwa masiku ambiri?+
נ [Nun]
ס [Samekh]
14 Siyani kuchita zinthu zoipa ndipo muzichita zabwino.+
Yesetsani kukhala mwamtendere ndi ena komanso kuulimbikitsa.+
ע [Ayin]
פ [Pe]
16 Koma Yehova amakwiyira anthu ochita zoipa,
Iye adzawawononga ndipo sadzakumbukiridwanso padziko lapansi.+
צ [Tsade]
ק [Qoph]
18 Yehova ali pafupi ndi anthu a mtima wosweka.+
Iye amapulumutsa anthu amene akudzimvera chisoni mumtima mwawo.*+
ר [Resh]
ש [Shin]
20 Amateteza mafupa onse a munthu wolungamayo.
Ndipo palibe fupa ngakhale limodzi limene lathyoledwa.+
ת [Taw]
21 Munthu woipa adzakumana ndi tsoka ndipo adzafa.
Anthu odana ndi munthu wolungama adzapezeka olakwa.
22 Yehova amawombola moyo wa atumiki ake.
Palibe aliyense wothawira kwa iye amene adzapezeke wolakwa.+