Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • nwt Micah 1:1-7:20
  • Mika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mika
  • Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
Mika

MIKA

1 Yehova analankhula ndi Mika*+ wa ku Morese mʼmasiku a Yotamu,+ Ahazi+ ndi Hezekiya,+ mafumu a Yuda.+ Analankhula naye kudzera mʼmasomphenya ndipo anamuuza zokhudza Samariya ndi Yerusalemu kuti:

 2 “Tamverani anthu nonsenu!

Mvetsera mwatcheru iwe dziko lapansi ndi zonse zili mmenemo.

Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa akhale mboni yokutsutsani,+

Yehova akutsutseni ali mʼkachisi wake woyera.

 3 Tamverani! Yehova akuchoka pamalo ake,

Ndipo atsika nʼkupondaponda malo okwezeka apadziko lapansi.

 4 Mapiri adzasungunuka kumapazi ake,+

Ndipo zigwa zidzagawanika,

Ngati phula losungunuka ndi moto.

Ndipo zidzayenda ngati madzi othiridwa pamalo otsetsereka.

 5 Zonsezi zidzachitika chifukwa chakuti Yakobo wandigalukira.

Ndiponso chifukwa cha machimo a nyumba ya Isiraeli.+

Kodi wachititsa kuti Yakobo andigalukire ndani?

Kodi si anthu a ku Samariya?+

Wachititsa ndani kuti Yuda akhale ndi malo okwezeka?+

Si anthu a ku Yerusalemu kodi?

 6 Samariya ndidzamusandutsa bwinja,

Malo oyenera kudzalapo mpesa.

Miyala yake ndidzaiponya* mʼchigwa.

Ndipo maziko ake ndidzawafukula nʼkuwasiya pamtunda.

 7 Zifaniziro zake zonse zogoba zidzaphwanyidwa nʼkukhala zidutswazidutswa.+

Ndipo mphatso zonse zimene ankalandira ngati malipiro zidzatenthedwa pamoto.+

Mafano ake onse ndidzawawononga.

Chifukwa anawapeza kuchokera ku ndalama zimene ankalandira pochita uhule.

Ndipo tsopano zinthu zimenezi zidzatengedwa kuti zikakhale malipiro a mahule kwinakwake.”

 8 Chifukwa cha zimenezi ndidzalira ndi kufuula.+

Ndidzayenda wopanda nsapato komanso wosavala.+

Ndidzalira ngati mimbulu,

Ndiponso ngati nthiwatiwa.

 9 Bala lake ndi losachiritsika,+

Ndipo lakafika mpaka ku Yuda.+

Mliri umenewu wafalikira mpaka kukafika pageti la anthu amtundu wanga ku Yerusalemu.+

10 “Musanene zimenezi ku Gati.

Ndipo musalire ngakhale pangʼono.

Gubudukani pafumbi ku Beti-afira.*

11 Inu anthu a ku Safiri, tulukani mʼdziko lanu muli maliseche ndiponso mukuchititsa manyazi.

Anthu a ku Zaanana sanachoke mʼdziko lawo.

Ku Beti-ezeli kuzingomveka kulira kokhakokha ndipo anthu ake adzasiya kukuthandizani.

12 Anthu a ku Maroti ankayembekezera zinthu zabwino,

Koma zoipa zochokera kwa Yehova zafika pageti la ku Yerusalemu.

13 Inu anthu a ku Lakisi, mangirirani galeta ku gulu la mahatchi.*+

Ndinu amene munayambitsa tchimo la mwana wamkazi wa Ziyoni,*

Popeza kugalukira kwa Isiraeli kunapezeka mwa inu.+

14 Choncho mudzapereka mphatso zotsanzikirana kwa Moreseti-gati.

Anthu a ku Akizibu+ anapusitsa mafumu a Isiraeli.

15 Inu anthu a ku Maresha+ ndidzakubweretserani munthu wokugonjetsani,*+

Ulemerero wa Isiraeli udzafika mpaka ku Adulamu.+

16 Muchotse tsitsi lonse ndipo mumete mpala chifukwa cha ana anu amene mumawakonda.

Metani mpala ngati wa chiwombankhanga,

Chifukwa chakuti ana anuwo atengedwa kupita kudziko lina.”+

2 “Tsoka kwa anthu amene amakonza chiwembu,

Amene akagona pabedi pawo, amaganizira kuti achite zoipa.

Ndipo mʼmawa kukacha, amazichitadi.

Chifukwa ali ndi mphamvu zochitira zimenezo.+

 2 Iwo amalakalaka minda ya anthu ena ndipo amaitenga.+

Amalakalakanso nyumba za anthu ena nʼkuzitenga.

Amatenga mwachinyengo nyumba ya munthu,+

Ndipo amatenganso cholowa cha munthu.

 3 Choncho Yehova wanena kuti:

‘Ndikukonza zobweretsa tsoka+ pa banja ili, tsoka limene simudzatha kulithawa.+

Anthu inu simudzayendanso modzikuza+ chifukwa idzakhala nthawi ya tsoka.+

 4 Pa tsikulo anthu adzanena mwambi wokhudza anthu inu.

Ndipo adzaimba nyimbo yokulirirani.+

Adzanena kuti: “Ife ndiye tatha basi!+

Wachititsa kuti cholowa cha anthu amtundu wathu chiperekedwe kwa anthu ena. Talandidwa cholowa chathu.+

Iye wapereka minda yathu kwa anthu osakhulupirika.”

 5 Choncho simudzapezeka aliyense woyeza malo ndi chingwe,

Amene azidzagawa malo mumpingo wa Yehova.

 6 Amanena kuti: “Siyani kulalikira!

Musalalikirenso zokhudza zinthu zimenezi.

Sitidzachititsidwa manyazi.”

 7 Inu a mʼnyumba ya Yakobo, kodi mukunena kuti:

“Kodi mzimu wa Yehova sukuleza mtima?

Kodi zochita zake ndi zimenezi?”

Kodi mawu anga sapindulitsa anthu owongoka mtima?

 8 Posachedwapa anthu anga enieni andiukira ngati mdani wanga.

Anthu amene akuyenda molimba mtima, ngati anthu obwera kuchokera kunkhondo,

Mumawavula mkanjo wawo wokongola kwambiri umene avala pamwamba pa zovala zawo.

 9 Inu mwathamangitsa akazi amtundu wanga mʼnyumba zawo zabwino kwambiri.

Mwalanda ana awo zinthu zabwino zimene ndinawadalitsa nazo ndipo simudzazibwezanso mpaka kalekale.

10 Nyamukani muzipita, chifukwa malowa si opumulirako.

Popeza dzikoli ndi lodetsedwa+ liwonongedwa, ndipo liwonongedwa koopsa.+

11 Munthu akatsatira zinthu zopanda pake ndi zachinyengo nʼkunena bodza lakuti:

“Ndidzakulalikirani zokhudza vinyo ndi chakumwa choledzeretsa,”

Adzangokhala mlaliki wa anthu awa.+

12 Ndithu ndidzasonkhanitsa mbadwa zonse za Yakobo.

Ndidzasonkhanitsa Aisiraeli otsala.+

Ndidzawabweretsa pamalo amodzi ngati gulu la nkhosa mʼkhola,

Komanso ngati gulu la ziweto pamalo amsipu.+

Kumeneko kudzakhala phokoso la anthu.’+

13 Wogumula mpanda adzawatsogolera.

Iwo adzakulitsa pogumulidwapo nʼkudutsa pageti.+

Mfumu yawo idzakhala patsogolo pawo

Ndipo Yehova adzawatsogolera.”+

3 Ine ndinati: “Tamverani inu atsogoleri a mbadwa za Yakobo

Ndiponso inu olamulira a nyumba ya Isiraeli.+

Kodi simukuyenera kudziwa chilungamo?

 2 Koma mumadana ndi zinthu zabwino+ ndipo mumakonda zinthu zoipa.+

Mumasenda khungu la anthu anga nʼkuchotsa mnofu pamafupa awo.+

 3 Mumadyanso mnofu wa anthu anga,+

Ndipo mumasenda khungu lawo.

Mumaswa mafupa awo nʼkuwaphwanyaphwanya.+

Ngati zinthu zimene zaphikidwa mumphika* komanso ngati nyama imene ili mumphika.

 4 Pa nthawiyo adzafuulira Yehova kuti awathandize,

Koma sadzawayankha.

Adzawabisira nkhope yake pa nthawi imeneyo,+

Chifukwa cha zochita zawo zoipa.+

 5 Izi nʼzimene Yehova wanena zomwe zidzachitikire aneneri amene akusocheretsa anthu a mtundu wanga.+

Amene amalengeza kuti ‘Mtendere!’+ kwinaku akuluma ndi mano awo.*+

Koma munthu akapanda kuika chakudya mʼkamwa mwawo, amakonzekera zokamenyana naye:

 6 ‘Usiku udzakufikirani,+ koma simudzaona masomphenya.+

Kuzidzakhala mdima, koma inu simudzaloseranso.

Aneneri amenewa dzuwa lidzawalowera.

Ndipo mdima udzawagwera masanasana.+

 7 Oona masomphenya adzachititsidwa manyazi,+

Ndipo olosera adzakhumudwa.

Onsewa adzaphimba ndevu zawo zapamulomo,*

Chifukwa Mulungu sadzawayankha.’”

 8 Koma ine ndapatsidwa mphamvu ndi mzimu wa Yehova.

Ndipo ndine wokonzeka kuchita chilungamo ndiponso kusonyeza mphamvu,

Kuti ndiuze mbadwa za Yakobo za kugalukira kwawo, komanso Isiraeli za tchimo lake.

 9 Tamverani izi inu atsogoleri a nyumba ya Yakobo

Komanso inu olamulira a nyumba ya Isiraeli,+

Amene mumadana ndi chilungamo ndiponso mumapotoza zinthu zonse zowongoka,+

10 Inu amene mumapha anthu kuti mumange Ziyoni ndiponso mumachita zinthu zopanda chilungamo kuti mumange Yerusalemu.+

11 Atsogoleri amumzindawo saweruza asanalandire ziphuphu,+

Ansembe ake amaphunzitsa kuti apeze malipiro,+

Ndipo aneneri ake amalosera kuti apeze ndalama.+

Komatu iwo amanena kuti amadalira Yehova ndipo amati:

“Yehovatu ali nafe,+

Ndipo tsoka silidzatigwera.”+

12 Choncho chifukwa cha anthu inu,

Ziyoni adzalimidwa ngati munda,

Yerusalemu adzakhala mabwinja.+

Ndipo phiri la nyumba* ya Mulungu lidzakhala ngati zitunda zamunkhalango.+

4 Mʼmasiku otsiriza,

Phiri la nyumba ya Yehova+

Lidzakhazikika pamwamba penipeni pa mapiri akuluakulu,

Ndipo lidzakwezedwa kupitirira mapiri angʼonoangʼono.

Anthu a mitundu yosiyanasiyana adzapita kumeneko.+

 2 Anthu ochokera mʼmitundu yosiyanasiyana adzabwera nʼkunena kuti:

“Bwerani, tiyeni tipite kuphiri la Yehova,

Tipite kunyumba ya Mulungu wa Yakobo.+

Iye akatiphunzitsa njira zake,

Ndipo ife tidzayenda mʼnjira zakezo.”

Chifukwa chilamulo,* chidzaphunzitsidwa mu Ziyoni

Ndipo mawu a Yehova adzaphunzitsidwa mu Yerusalemu.

 3 Mulungu adzaweruza mitundu yambiri ya anthu,+

Ndipo adzakonza zinthu zolakwika zokhudza anthu ochokera mʼmitundu yamphamvu yakutali.

Iwo adzasula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo,

Ndiponso mikondo yawo kuti ikhale zida zosadzira mitengo.+

Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake,

Ndipo anthuwo sadzaphunziranso nkhondo.+

 4 Aliyense adzakhala pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa mkuyu,+

Ndipo sipadzakhala wowaopseza,+

Chifukwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena zimenezi.

 5 Anthu a mtundu uliwonse adzayenda mʼdzina la mulungu wawo.

Koma ife tidzayenda mʼdzina la Yehova Mulungu+ wathu mpaka kalekale.

 6 Yehova wanena kuti, “Pa tsiku limenelo,

Ndidzasonkhanitsa anthu amene ankayenda motsimphina.

Ndidzasonkhanitsanso anthu amene anamwazikana,+

Komanso anthu amene ndinawalanga.

 7 Anthu amene ankayenda motsimphina, ndidzawasonkhanitsanso ngati anthu otsala.+

Anthu amene anachotsedwa mʼdziko lawo nʼkupita kutali, ndidzawasandutsa mtundu wamphamvu.+

Ndipo Yehova adzakhala mfumu yawo mʼphiri la Ziyoni,

Kuyambira panopa mpaka kalekale.

 8 Koma iwe nsanja ya gulu la nkhosa,

Malo okwera a mwana wamkazi wa Ziyoni,*+

Ulamuliro udzabwerera. Ulamuliro woyamba udzabwerera kwa iwe,+

Ufumu wa mwana wamkazi wa Yerusalemu.*+

 9 Ndiye nʼchifukwa chiyani ukufuula kwambiri?

Kodi ulibe mfumu?

Kapena alangizi ako awonongedwa?

Moti ukumva zowawa ngati mkazi amene akubereka?+

10 Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni udzamva ululu woopsa,

Ngati mkazi amene akubereka.

Chifukwa tsopano uchoka mʼtauni nʼkupita kukakhala kumudzi.

Ukafika mpaka ku Babulo,+

Ndipo kumeneko udzapulumutsidwa.+

Kumeneko Yehova adzakuwombola mʼmanja mwa adani ako.+

11 Anthu amitundu yosiyanasiyana adzasonkhana kuti akuukire.

Anthuwo adzanena kuti, ‘Tiyeni timuwononge,

Ndipo maso athu aone zimenezi zikuchitikira Ziyoni.’

12 Koma iwo sakudziwa maganizo a Yehova.

Iwo sakumvetsa cholinga chake.

Chifukwa adzawasonkhanitsa pamalo opunthira mbewu ngati mmene amasonkhanitsira tirigu amene angomumweta kumene.

13 Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni, nyamuka upunthe tirigu.+

Chifukwa nyanga zako ndidzazisandutsa chitsulo.

Ziboda zako ndidzazisandutsa kopa.*

Ndipo udzanyenyanyenya mitundu yambiri ya anthu.+

Phindu limene iwo apeza mwachinyengo, udzalipereka kwa Yehova.

Ndipo zinthu zawo udzazipereka kwa Ambuye woona wa dziko lonse lapansi.”+

5 “Iwe mzinda umene waukiridwa,

Tsopano ukudzichekacheka.

Adani atizungulira kuti atiukire.+

Iwo amenya woweruza wa Isiraeli patsaya ndi ndodo.+

 2 Iwe Betelehemu Efurata,+

Mzinda waungʼono kwambiri moti sungawerengedwe ngati umodzi mwa mizinda ya fuko la Yuda,

Mwa iwe mudzatuluka munthu amene ndidzamusankhe kuti akhale wolamulira mu Isiraeli.+

Munthu ameneyu wakhala alipo kuyambira kalekale, wakhala alipo kuyambira masiku akale.

 3 Choncho Mulungu adzawasiya Aisiraeli,

Mpaka pamene mkazi amene adzabereke, atabereka.

Ndipo abale ake onse a munthuyo adzabwerera kwa Aisiraeli.

 4 Iye adzaimirira nʼkuyamba kuweta nkhosa mothandizidwa ndi mphamvu za Yehova,+

Ndiponso mʼdzina lalikulu la Yehova Mulungu wake.

Anthu azidzakhala motetezeka,+

Ndipo mphamvu zake zidzafika mpaka kumalekezero a dziko lapansi.+

 5 Iye adzabweretsa mtendere.+

Asuri akadzalowa mʼdziko lathu, akadzaponda nsanja zathu zolimba,+

Tidzawatumizira abusa 7, inde atsogoleri* 8 a anthu kuti akathane nawo.

 6 Atsogoleriwo adzalanga dziko la Asuri ndi lupanga,+

Komanso dziko la Nimurodi+ mʼnjira zake zonse zolowera mʼdzikolo.

Wolamulirayo adzatipulumutsa kwa Asuri,+

Asuriwo akadzangofika mʼdziko lathu nʼkuponda nthaka yathu.

 7 Mbadwa zotsala za Yakobo zidzakhala pakati pa mitundu yambiri ya anthu,

Ngati mame ochokera kwa Yehova.

Komanso ngati mvula yowaza imene ikugwa pazomera,

Yomwe sidalira munthu

Kapena kuyembekezera ana a anthu.

 8 Mbadwa zotsala za Yakobo zidzakhala pakati pa mitundu yambiri ya anthu.

Zidzakhala pakati pa anthu ambiri.

Ngati mkango pakati pa nyama zakutchire.

Komanso ngati mkango wamphamvu pakati pa magulu ankhosa,

Umene umadutsa pakati pa nkhosazo nʼkuzimbwandira ndiponso kuzikhadzula

Ndipo palibe wozipulumutsa.

 9 Dzanja lanu lidzakhala pamwamba pa adani anu,

Ndipo adani anu onse adzaphedwa.”

10 Yehova wanena kuti, “Pa tsiku limenelo,

Ndidzapha mahatchi* anu ndipo magaleta anu ndidzawawononga.

11 Ndidzagwetsa mizinda yamʼdziko lanu.

Ndipo ndidzagumula malo anu onse okhala ndi mipanda yolimba kwambiri.

12 Ndidzathetsa zamatsenga zonse zimene mukuchita,

Ndipo pakati panu sipadzapezekanso wochita zamatsenga.+

13 Ndidzagwetsa zifaniziro zogoba ndi zipilala zopatulika zimene muli nazo,

Ndipo simudzagwadiranso ntchito za manja anu.+

14 Ndidzazula mizati* yanu yopatulika,+

Nʼkuwononga mizinda yanu.

15 Ndidzabwezera mokwiya ndiponso mwaukali

Anthu a mitundu imene sinandimvere.”

6 Imvani zimene Yehova akunena.

Nyamukani mukanene mlandu wanu kwa mapiri akuluakulu,

Ndipo mapiri angʼonoangʼono akamve mawu anu.+

 2 Inu mapiri akuluakulu, imvani mlandu umene Yehova ali nawo pa anthu ake.

Mvetserani inu maziko a dziko lapansi,+

Chifukwa Yehova ali ndi mlandu ndi anthu ake.

Iye azenga mlandu Aisiraeli, kuti:+

 3 “Inu anthu anga, ndakulakwirani chiyani?

Kodi ndachita chiyani kuti ndikutopetseni?+

Perekani umboni wonditsutsa.

 4 Ine ndinakutulutsani mʼdziko la Iguputo,+

Ndinakuwombolani mʼnyumba ya ukapolo,+

Ndipo ndinakutumizirani Mose, Aroni ndi Miriamu kuti akutsogolereni.+

 5 Inu anthu anga, chonde kumbukirani zimene Balaki mfumu ya Mowabu ankafuna kuchita.+

Ndiponso zimene Balamu mwana wa Beori anamuyankha.+

Kumbukirani zimene zinachitika kuyambira ku Sitimu+ kukafika ku Giligala.+

Kumbukirani zimenezi kuti mudziwe ntchito zolungama za Yehova.”

 6 Kodi nditenge chiyani popita kwa Yehova?

Ndikagwade ndi chiyani kwa Mulungu wakumwamba?

Kodi ndipite nditatenga nsembe zopsereza zathunthu?

Ndiponso ana a ngʼombe achaka chimodzi?+

 7 Kodi Yehova adzasangalala ndi masauzande a nkhosa zamphongo?

Kodi adzakondwera ndi mitsinje ya mafuta masauzande ambirimbiri?+

Kodi ndipereke mwana wanga wamwamuna woyamba chifukwa cha zolakwa zanga,

Ndipereke chipatso cha mimba yanga chifukwa cha tchimo langa?+

 8 Iye anakuuza munthu iwe zimene zili zabwino.

Kodi Yehova akufuna kuti uzichita* chiyani?

Iye akungofuna kuti uzichita chilungamo,*+ uziona kuti kukhulupirika nʼkofunika,*+

Ndiponso uziyenda modzichepetsa+ ndi Mulungu wako.+

 9 Mawu a Yehova akumveka mumzinda.

Anthu anzeru zopindulitsa adzaopa dzina lanu.

Mverani mawu a ndodo ndi a amene anaisankha.*+

10 Kodi mʼnyumba ya munthu woipa mukupezekabe chuma chopezedwa mopanda chilungamo?

Ndiponso muyezo woperewera wa efa* umene ndi wonyansa?

11 Kodi ndingakhale woyera* ndili ndi sikelo yachinyengo,

Ndiponso thumba la miyala yachinyengo yoyezera zinthu?+

12 Anthu olemera amumzindawo amakonda kuchita zachiwawa.

Anthu ake amalankhula zabodza+

Ndipo lilime lawo ndi lachinyengo.+

13 “Choncho ine ndidzakumenyani mpaka mudzakhala ndi mabala,+

Ndipo mudzasautsika chifukwa cha machimo anu.

14 Inu mudzadya, koma simudzakhuta.

Ndipo mudzamvabe njala.+

Mudzanyamula zinthu kuti mukazisunge pabwino, koma simudzatha kuziteteza.

Zimene mudzatenge, ndidzazipereka kwa adani anu kuti aziwononge.

15 Mudzadzala mbewu, koma simudzakolola.

Mudzaponda maolivi, koma simudzagwiritsa ntchito mafuta ake.

Mudzapanga vinyo watsopano, koma simudzamwa vinyo.+

16 Mukutsatira malamulo a Omuri komanso zinthu zonse zimene anthu a mʼnyumba ya Ahabu amachita.+

Ndipo mukuyendera malangizo awo.

Nʼchifukwa chake ndidzakusandutsani chinthu chodabwitsa,

Ndipo anthu amumzindawo adzakhala oyenera kuwaimbira mluzu.+

Inuyo mudzanyozedwa ndi anthu a mitundu ina.”+

7 Tsoka kwa ine, chifukwa ndili ngati munthu amene,

Nthawi yokolola zipatso zamʼchilimwe* itatha,

Komanso nthawi yokunkha mʼmunda umene akololamo mphesa itatha,

Sanapeze mphesa zoti adye.

Komanso nkhuyu zoyambirira zimene akulakalaka.

 2 Anthu okhulupirika atha padziko lapansi.

Pakati pa anthu palibe munthu wachilungamo.+

Onse amabisalira anzawo kuti akhetse magazi.+

Aliyense amasaka mʼbale wake ndi ukonde.

 3 Manja awo amachita zoipa ndipo amazichita bwino kwambiri.+

Kalonga amalamula kuti amupatse mphatso,

Woweruza amauza anthu kuti amupatse chiphuphu.+

Munthu wotchuka amauza anthu zimene akulakalaka,+

Ndipo onsewa amakonzera limodzi chiwembu.

 4 Munthu amene iwo amati ndi wabwino kwambiri, ali ngati minga,

Ndipo munthu amene amati ndi wachilungamo kwambiri, ndi woipa kuposa mpanda wa mitengo yaminga.

Tsiku limene alonda awo ananena komanso limene adzaweruzidwe lidzafika ndithu.+

Pa tsikulo iwo adzathedwa nzeru.+

 5 Musamakhulupirire anzanu.

Musamadalire mnzanu wapamtima.+

Muzisamala ndi zimene mumauza amene mumagona naye pafupi.

 6 Chifukwa mwana wamwamuna akunyoza bambo ake.

Mwana wamkazi akutsutsana ndi mayi ake,+

Ndipo mkazi wokwatiwa akutsutsana ndi apongozi ake aakazi.+

Adani ake a munthu ndi anthu a mʼbanja lake.+

 7 Koma ine ndidzayembekezera Yehova.+

Ndidzayembekezera moleza mtima Mulungu wa chipulumutso changa.+

Mulungu wanga adzandimvera.+

 8 Iwe mdani* wanga, usasangalale chifukwa cha zimene zandichitikira.

Ngakhale kuti ndagwa, ndidzadzuka.

Ngakhale kuti ndili mumdima, Yehova adzakhala kuwala kwanga.

 9 Ndidzapirira mkwiyo wa Yehova,

Chifukwa ndamuchimwira.+

Ndidzaupirira mpaka ataweruza mlandu wanga nʼkundichitira chilungamo.

Iye adzandipititsa pamalo owala,

Ndipo ndidzaona chilungamo chake.

10 Mdani wanga adzaonanso zimenezi,

Ndipo manyazi adzagwira amene ankandinena kuti:

“Yehova Mulungu wako ali kuti?”+

Maso anga adzamuyangʼana.

Iye adzapondedwapondedwa ngati matope amumsewu.

11 Lidzakhala tsiku lomanga mpanda wako wamiyala.

Pa tsiku limenelo malire adzakulitsidwa.*

12 Pa tsiku limenelo anthu adzabwera kwa iwe,

Ochokera kudziko la Asuri ndi kumizinda ya ku Iguputo.

Ochokera ku Iguputo mpaka ku Mtsinje.*

Komanso ochokera kunyanja ina mpaka kunyanja ina ndiponso kuphiri lina mpaka kuphiri linanso.+

13 Dzikoli lidzakhala bwinja chifukwa cha anthu okhala mmenemo,

Chifukwa cha zimene achita.*

14 Weta anthu ako ndi ndodo yako, gulu la nkhosa zomwe ndi cholowa chako,+

Zimene zinkakhala zokhazokha mʼnkhalango komanso pakati pa mitengo ya zipatso.

Uzilole zikadyere ku Basana ndi ku Giliyadi+ ngati mmene zinkachitira kale.

15 “Ndidzakusonyezani zinthu zodabwitsa,

Ngati mmene ndinachitira nthawi imene munkachokera ku Iguputo.+

16 Anthu a mitundu ina adzaona zodabwitsazo ndipo adzachita manyazi ngakhale kuti ndi amphamvu.+

Iwo adzagwira pakamwa,

Ndipo makutu awo adzagontha.

17 Adzanyambita fumbi ngati njoka.+

Ngati nyama zokwawa, adzatuluka akunjenjemera mʼmalo awo obisalamo.

Adzabwera kwa Yehova Mulungu akuchita mantha,

Ndipo adzayamba kukuopani.”+

18 Kodi pali Mulungu winanso wofanana ndi inu,

Amene amakhululukira zolakwa ndi machimo+ a anthu ake otsala omwe ndi cholowa chake?+

Inu simudzakhalabe wokwiya mpaka kalekale,

Chifukwa mumakonda chikondi chokhulupirika.+

19 Inu mudzatichitiranso chifundo+ ndipo mudzagonjetsa* zolakwa zathu.

Machimo athu onse mudzawaponya mʼnyanja pamalo ozama.+

20 Yakobo mudzamusonyeza kukhulupirika.

Abulahamu mudzamusonyeza chikondi chokhulupirika,

Ngati mmene munalumbirira kwa makolo athu kalekale.+

Chidule cha dzina lakuti Mikayeli (kutanthauza “Ndani Ali Ngati Mulungu”) kapena Mikaya (kutanthauza “Ndani Ali Ngati Yehova”).

Mʼchilankhulo choyambirira, “ndidzaikhuthulira.”

Kapena kuti, “mʼnyumba ya Afira.”

Ena amati “mahosi.”

Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu andakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.

Kapena kuti, “wolanda zinthu za ena.”

Kapena kuti, “mumphika wakukamwa kwakukulu.”

Mabaibulo ena amati, “pamene ali ndi choti atafune.”

Kapena kuti, “adzaphimba pakamwa pawo.”

Kapena kuti, “phiri la kachisi.”

Kapena kuti, “malangizo.”

Mawu akuti “mwana wamkazi wa Ziyoni” ndi mawu andakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.

Mawu akuti “mwana wamkazi wa Yerusalemu” ndi mawu andakatulo ndipo nthawi zambiri amanena za mzinda wa Yerusalemu kapena anthu amene ankakhala mumzindawo.

Kapena kuti, “mkuwa.”

Kapena kuti, “akalonga.”

Ena amati “mahosi.”

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.

Kapena kuti, “umubwezere.”

Kapena kuti, “ukhale wachilungamo.”

Kapena kuti, “uzikhala wokoma mtima ndipo chikondi chako chizikhala chokhulupirika.” Mʼchilankhulo choyambirira, “uzikonda chikondi chokhulupirika.”

Kapena kuti, “Mverani chilango ndi amene akuchipereka.”

Onani Zakumapeto B14.

Kapena kuti, “wosalakwa.”

Mawu akuti “zipatso za mʼchilimwe” makamaka amatanthauza nkhuyu ndipo nthawi zina amatanthauza zipatso za kanjedza.

Mawu a Chiheberi amene amasuliridwa kuti “mdani,” amanena za munthu wamkazi.

Mabaibulo ena amati, “Pa tsiku limenelo lamulo lidzakhala kutali.”

Umenewu ndi mtsinje wa Firate.

Mʼchilankhulo choyambirira, “Chifukwa cha chipatso cha ntchito zawo.”

Kapena kuti, “mudzapondaponda.”

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani