MUTU 35
Hana Anapempha Mwana Wamwamuna
Bambo wina wa ku Isiraeli dzina lake Elikana anali ndi akazi awiri. Mayina a akaziwo anali Hana ndi Penina. Koma Elikana ankakonda kwambiri Hana. Penina anali ndi ana ambiri koma Hana analibe ngakhale mmodzi. Chifukwa cha zimenezi, Penina ankanyoza Hana nthawi zonse. Chaka chilichonse, Elikana ankapita kukalambira Mulungu ku Silo limodzi ndi banja lake. Tsiku lina ali kumeneko, anazindikira kuti mkazi wake Hana, amene ankamukonda kambiri, wakhumudwa kwambiri. Iye anamuuza kuti: ‘Hana usalire. Ndimakukonda kwambiri. Kodi si ine woposa ana amene ukufunawo?’
Kenako Hana ananyamuka kupita kukapemphera. Iye anapempha Yehova kuti amuthandize ndipo ankapemphera uku akulira. Hana analonjeza kuti: ‘Yehova, mukandipatsa mwana wamwamuna ndidzakupatsani kuti azikutumikirani kwa moyo wake wonse.’
Mkulu wa ansembe dzina lake Eli ataona milomo ya Hana ikugwedera, anaganiza kuti waledzera. Koma Hana anayankha kuti: ‘Ayi, mbuyanga, inetu sindinaledzere. Ndili ndi vuto lalikulu kwambiri limene ndikufotokozera Yehova.’ Eli anazindikira kuti walakwitsa ndipo anauza Hanayo kuti: ‘Mulungu akupatse zimene ukufunazo.’ Zitatero Hana anayamba kumva bwino mumtima ndipo anabwerera. Chaka chisanathe, anabereka mwana n’kumupatsa dzina loti Samueli. Iye ayenera kuti anasangalala kwambiri.
Hana sanaiwale zimene analonjeza kwa Yehova. Samueli atangosiya kuyamwa, anamupereka kuti azikatumikira kuchihema. Iye anauza Eli kuti: ‘Mwana uyu ndi amene ndinkapempha nthawi ijayi. Ndamupereka kuti atumikire Yehova kwa moyo wake wonse.’ Chaka chilichonse, Elikana ndi Hana ankapita kukaona Samueli ndipo ankamutengera malaya atsopano odula manja. Yehova anapatsa Hana ana ena, aamuna atatu ndi aakazi awiri.
“Pitirizani kupempha ndipo adzakupatsani. Pitirizani kufunafuna ndipo mudzapeza.”—Mateyu 7:7