Nkhani Zimene Zili M’magaziniyi
MLUNGU WA OCTOBER 23-29, 2017
3 Tiziyesetsa Kukhala Odziletsa
Yehova ndi chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani yodziletsa. Kodi tingamutsanzire bwanji posonyeza khalidwe limeneli? Nanga n’chiyani chingatithandize kukhala odziletsa?
MLUNGU WA OCTOBER 30, 2017–NOVEMBER 5, 2017
8 Tizitsanzira Yehova pa Nkhani ya Chifundo
Kodi munthu angasonyeze bwanji chifundo? Yehova ndiponso Yesu ndi zitsanzo zabwino kwambiri pa nkhaniyi. Koma kodi tingawatsanzire bwanji? Nanga kuchita zimenezi kungatithandize bwanji ifeyo?
MLUNGU WA NOVEMBER 6-12, 2017
18 “Mawu a Mulungu Wathu Adzakhala Mpaka Kalekale”
MLUNGU WA NOVEMBER 13-19, 2017
23 ‘Mawu a Mulungu Ndi Amphamvu’
N’zolimbikitsa kwambiri kuti masiku ano Baibulo limapezeka m’zilankhulo zambiri. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timayamikira kuti Baibulo limapezeka m’chilankhulo chimene timachidziwa bwino? Nkhani ziwirizi zitithandiza kuyamikira kwambiri Baibulo komanso kukonda kwambiri Mulungu yemwe anatipatsa Baibulolo.
MLUNGU WA NOVEMBER 20-26, 2017
28 ‘Limba Mtima Ndipo Ugwire Ntchitoyi’
Akhristu amafunika kukhala olimba mtima. Kodi zitsanzo za anthu amene analimba mtima zingatithandize bwanji? Kodi achinyamata, makolo, alongo achikulire komanso abale obatizidwa angasonyeze bwanji kuti ndi olimba mtima komanso ofunitsitsa kugwira ntchito zabwino?