CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | MATEYU 25
“Khalanibe Maso”
Ngakhale kuti fanizo la anamwali 10 limanena za otsatira odzozedwa a Khristu, mfundo zake zimakhudza Akhristu onse. (w15 3/15 12-16) Iye anati, “Khalanibe maso chifukwa simukudziwa tsiku kapena ola lake.” (Mat. 25:13) Kodi mungakwanitse kufotokoza bwinobwino fanizoli?
- Mkwati (vesi 1)—Yesu 
- Anamwali ochenjera omwe anakonzekera (vesi 2)—Akhristu odzozedwa omwe ndi okonzeka kugwira ntchito yawo mokhulupirika ndipo adzawala ngati zounikira mpaka m’nthawi yamapeto. (Afil. 2:15) 
- Mawu ofuula akuti: “Mkwati uja wafika!” (vesi 6)—Chizindikiro cha kukhalapo kwa Yesu 
- Anamwali opusa (vesi 8)—Akhristu odzozedwa omwe anapita kukachingamira mkwati koma analephera kukhalabe maso ndipo analephera kukhalabe okhulupirika 
- Anamwali ochenjera anakana kugawana mafuta awo ndi anamwali opusa (vesi 9)—Pambuyo poti Yehova wadinda chidindo chomaliza Akhristu odzozedwa, zidzakhala zosatheka kuti odzozedwa okhulupirikawa athandize osakhulupirika aja 
- “Mkwati anafika” (vesi 10)—Yesu adzabwera kudzapereka chiweruzo chakumapeto kwa chisautso chachikulu 
- Anamwali ochenjera analowa limodzi ndi mkwati m’nyumba imene munali phwando laukwati, ndipo chitseko chinatsekedwa (vesi 10)—Yesu adzasonkhanitsa odzozedwa okhulupirika n’kupita nawo kumwamba, koma osakhulupirika sadzalandira nawo mphoto imeneyi