MAWU A M’BAIBULO
Kukhululuka Machimo Amene Anachitika Kale
Njira yokhayo imene machimo athu angakhululukidwe ndi kudzera mu nsembe imene Yesu anapereka pogwiritsa ntchito magazi ake. (Aef. 1:7) Komabe Baibulo limati: “Mulungu . . . anachita zimenezi pofuna kuonetsa chilungamo chake chifukwa anasonyeza kuti ndi wosakwiya msanga pokhululuka machimo amene anachitika kale,” kutanthauza Yesu asanapereke dipo. (Aroma 3:25) Koma kodi Yehova anachita bwanji zimenezi pa nthawi imodzimodziyo n’kusonyeza chilungamo chake?
Kwa Yehova zinali ngati dipo laperekedwa kale kungochokera pamene anaganiza zosankha “mbadwa” yoti idzapulumutse anthu. (Gen. 3:15; 22:18) Mulungu sankakayikira ngakhale pang’ono kuti pa nthawi yake, Mwana wake wokondedwa adzapereka moyo wake monga dipo. (Agal. 4:4; Aheb. 10:7-10) Mulungu anapatsa Yesu mphamvu zotha kukhululuka machimo ngakhale pamene dipo linali lisanaperekedwe. Yesu ankakhululukira anthu omwe anasonyeza kuti anali ndi chikhulupiriro chifukwa ankadziwa kuti dipo lomwe adzapereke lidzaphimba machimo awo.—Mat. 9:2-6.