Mfundo Zina Zothandiza Mabanja
BAIBULO LIMAPEREKA MALANGIZO OTHANDIZA KWAMBIRI kwa anthu okwatirana, makolo komanso kwa achinyamata. Malangizo ake angakuthandizeni kukhala oganiza bwino komanso kusankha bwino zochita.—Miyambo 1:1-4.
BAIBULO LIMAYANKHANSO MAFUNSO OFUNIKA KWAMBIRI MONGA:
- Kodi cholinga cha moyo n’chiyani? 
- Kodi Mulungu ndi amene amachititsa kuti tizivutika? 
- Kodi chimachitika n’chiyani tikamwalira? 
Tikukulimbikitsani kuti mufufuze m’Baibulo mayankho a mafunso amenewa komanso ena. Onerani kavidiyo kakuti, N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? popanga sikani kachidindo aka kapena pitani pa www.pr2711.com/ny.