Kodi N’chiyani Chingathandize Kuti Banja Likhale Losangalala?
Kodi mukuganiza kuti ndi . . .
- chikondi? 
- ndalama? 
- kapena zinthu zina? 
ZIMENE BAIBULO LIMANENA
“Odala [kapena kuti osangalala] ndi amene akumva mawu a Mulungu ndi kuwasunga!”—Luka 11:28, Baibulo la Dziko Latsopano.
KODI ZIMENEZI ZIKUTANTHAUZA CHIYANI?
Zikutanthauza kuti malangizo a m’Baibulo angathandize banja lanu kukhala ndi chikondi chenicheni. —Aefeso 5:28, 29.
Kulemekezana.—Aefeso 5:33.
Kukhulupirirana.—Maliko 10:6-9.
KODI ZIMENE BAIBULO LIKUNENAZI TINGAZIKHULUPIRIREDI?
Inde, tingazikhulupirire pa zifukwa ziwiri izi:
- Mulungu ndi amene anayambitsa banja. Baibulo limanena kuti Yehova Mulungu ndi amene amapangitsa “banja lililonse . . . kukhala ndi dzina.” (Aefeso 3:14, 15) M’mawu ena tinganene kuti mabanja alipo chifukwa Yehova ndi amene anapangitsa kuti akhalepo. Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani? - Taganizirani izi: Mutakhala kuti mukudya chakudya chinachake chokoma ndipo mukufuna kudziwa kaphikidwe kake, kodi mungafunse ndani? N’zodziwikiratu kuti mungafunse amene waphika chakudyacho. - N’chimodzimodzinso ndi banja. Kuti tikhale ndi banja losangalala tiyenera kupeza malangizo a Yehova yemwe anayambitsa banja.—Genesis 2:18-24. 
- Mulungu amakuderani nkhawa. Mabanja anzeru amayesetsa kufufuza malangizo ochokera kwa Yehova omwe amapezeka m’Baibulo. N’chifukwa chiyani tikutero? N’chifukwa chakuti ‘iye amatidera nkhawa.’ (1 Petulo 5:6, 7) Yehova amatifunira zabwino kwambiri ndipo malangizo amene amatipatsa amakhala othandiza nthawi zonse.—Miyambo 3:5, 6; Yesaya 48:17, 18. 
GANIZIRANI MFUNDO IYI
Kodi mungatani kuti mukhale mwamuna, mkazi kapena kholo labwino?
Baibulo limayankha funso limeneli pa AEFESO 5:1, 2 ndi pa AKOLOSE 3:18-21.