NYIMBO 36
Titeteze Mitima Yathu
zosindikizidwa
	- 1. Titeteze mtima wathu - Tikhale ndi moyo. - M’lungu amadziwa bwino - Za mumtima mwathu. - Mtima ndi wonyenga - Ungamatisocheretse. - Choncho tiganize bwino - Timvere Yehova. 
- 2. Timafunafuna M’lungu - Tikamapemphera. - Timathokozadi zonse - Zomwe amachita. - Zomwe amatiphunzitsa - Timazitsatira - Ndipo tikhulupirike, - Timusangalatse. 
- 3. Titeteze mtima wathu - Tipewe zoipa. - Mawu a Yehova M’lungu - Atitsogolere. - Anthu okhulupirika - Amawakondadi. - Choncho tizimulambira - Monga bwenzi lathu. 
(Onaninso Sal. 34:1; Afil. 4:8; 1 Pet. 3:4.)