NYIMBO 121
Timafunika Kukhala Odziletsa
zosindikizidwa
1. Timakonda Yehova kwambiri
Koma poti ndife anthu ochimwa,
Timafunika kudziletsa.
Mzimu umatithandizadi.
2. Tsiku ndi tsiku timayesedwa.
Uchimowu ungatisocheretse
Koma choonadi n’champhamvu.
Yehova amatithandiza.
3. Tilemekeze dzina la M’lungu
Muzochita ndiponso zolankhula.
Cholinga chathu chiyenera
Kukhala anthu odziletsa.
(Onaninso 1 Akor. 9:25; Agal. 5:23; 2 Pet. 1:6.)