NYIMBO 122
Khalani Olimba Komanso Osasunthika
zosindikizidwa
(1 Akorinto 15:58)
1. Anthu akuvutika kwambiri
Ndipo akuopa zam’tsogolo.
Ife tilimbe tisasunthike
Potumikira M’lungu.
(KOLASI)
Tiyenera kulimba.
Tisiyane ndi dziko.
Tikhale olimba.
Tidzapeza moyo.
2. Misampha ndi yambiri m’dzikoli
Koma tingaipewe mwanzeru.
Tikamadanatu ndi zoipa
Sitidzasunthikadi.
(KOLASI)
Tiyenera kulimba.
Tisiyane ndi dziko.
Tikhale olimba.
Tidzapeza moyo.
3. Tizilambira Yehova yekha.
Tim’tumikire ndi mtima wonse.
Tizilalikiradi mwakhama.
Mapeto akubwera.
(KOLASI)
Tiyenera kulimba.
Tisiyane ndi dziko.
Tikhale olimba.
Tidzapeza moyo.
(Onaninso Luka 21:9; 1 Pet. 4:7.)