NYIMBO 124
Tizikhulupirika Nthawi Zonse
zosindikizidwa
	- 1. Tikhulupirike zedi, - Kwa M’lungu ndi kum’konda. - Malamulo ake onse, - Tifuna kuwadziwa. - Timapindula kwambiri, - Tikamamvera iye. - Ndi wokhulupirikadi, - Ndipo sitingam’siye. 
- 2. Tikhulupirike zedi, - Kwa abale mumpingo. - Nthawi zonse pamavuto, - Amatisamalira. - Tiziwalemekezatu - Kuchokera mumtima. - Tiwamvere nthawi zonse, - Ndipo tisawasiye. 
- 3. Tikhulupirike zedi - Tikamalangizidwa. - Ndi abale amumpingo, - Tifunika kumvera. - Ndipo Yehova Mulungu - Adzatidalitsatu, - Tikakhulupirikadi, - Iye adzatikonda. 
(Onaninso Sal. 149:1; 1 Tim. 2:8; Aheb. 13:17.)