NYIMBO 162
Zosowa Zanga Zauzimu
- 1. Tonsefe tilitu ndi - Zosowa za uzimu. - Timafuna kudziwatu - Mulungu woona. - Anthu amafufuza, - Mayankho alipotu. - M’mawu ake, M’Baibulo. - Tiziwawerenga. - (KOLASI) - Ine ndimutamanda. - Ndizimvera mawu ake. - Ndipo ndim’tumikira. - Andisamalira. - Ndipitiliza - Kukhala mnzake. 
- 2. Ndizipezabe nthawi - Yowerenga mawuwo, - N’kumapeza zinthu zomwe - Ndingamasinthebe. - Ena safuna kumva. - Ndiziwapempherera - Kuti nawo amudziwe, - N’kumuyandikira. - (KOLASI) - Ine ndimutamanda. - Ndizimvera mawu ake. - Ndipo ndim’tumikira. - Andisamalira. - Ndipitiliza - Kukhala mnzake. - Ine ndimutamanda. - Ndizimvera mawu ake. - Ndipo ndim’tumikira. - Andisamalira. - Ndipitiliza - Kukhala mnzake. - Ine ndimutamanda. - Ndizimvera mawu ake. - Ndipo ndim’tumikira. - Andisamalira. - Ndipitiliza - Kukhala mnzake. 
(Onaninso Mat. 5:6; 16:24; Yes. 40:8; Sal. 1:1, 2; 112:1; 119:97; 2 Tim. 4:4.)