CHUMA CHOPEZEKA M’MAWU A MULUNGU | GENESIS 25-26
Esau Anagulitsa Ukulu Wake
Esau ‘sanayamikire zinthu zopatulika.’ (Ahe 12:16) Iye anagulitsa ukulu wake ndipo kenako anakwatira akazi awiri achikunja.—Ge 26:34, 35.
DZIFUNSENI KUTI: ‘Kodi ndingasonyeze bwanji kuti ndimayamikira zinthu zopatulika zotsatirazi?’
- Ubwenzi wanga ndi Yehova 
- Mzimu woyera 
- Kudziwika ndi dzina loyera la Yehova 
- Ntchito yolalikira 
- Misonkhano 
- Ukwati