Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • mwb20.05 3
  • Kodi Mwakonzekera?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mwakonzekera?
  • Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
  • Nkhani Yofanana
  • Khalanibe Okonzeka Pamene Tili Kumapeto kwa “Masiku Otsiriza”
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2021
  • Kodi Mwakonzeka Kukumana Ndi Zachiwawa?
    Kabuku ka Msonkhano wa Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2022
  • Muzithandiza Ena Kupirira pa Nthawi Zovuta
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2022
  • Mmene Tingathandizire Pakachitika Ngozi Zadzidzidzi
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
Onani Zambiri
Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2020
mwb20.05 3
Banja likupakira zinthu zomwe angadzagwiritse ntchito pakadzachitika ngozi zogwa mwadzidzidzi.

MOYO WATHU WACHIKHRISTU

Kodi Mwakonzekera?

Ngati m’dera lanu mutachitika ngozi zogwa mwadzidzidzi, kodi ndinu wokonzeka? Zivomezi, mphepo zamkuntho, moto wa m’nkhalango, komanso madzi osefukira zikhoza kuchitika mwadzidzidzi ndipo zikhoza kuwononga zinthu kwambiri. Kuwonjezera pamenepo, zauchigawenga, zipolowe, komanso miliri zikhoza kuchitika kwina kulikonse mosayembekezeka. (Mlal. 9:11) Tisamaganize kuti zinthu ngati zimenezi sizingachitike m’dera limene tikukhala.

Aliyense ayenera kuchita zinazake pokonzekera ngozi zogwa mwadzidzidzi. (Miy. 22:3) Ngakhale kuti gulu la Yehova limapereka chithandizo pakachitika ngozi zogwa mwadzidzidzi, zimenezi sizikutanthauza kuti patokha tilibe udindo wochitapo kanthu.​—Agal. 6:5.

ONERANI VIDIYO YAKUTI ZIMENE TINGACHITE POKONZEKERA MASOKA ACHILENGEDWE NDIPO KENAKO YANKHANI MAFUNSO OTSATIRAWA:

  • M’bale akukonzekera mwauzimu ngozi zogwa mwadzidzidzi mwa kuwerenga Baibulo.

    Kodi tingakonzekere bwanji mwauzimu masoka asanachitike?

  • Chikwama, manambala a foni, foni.

    N’chifukwa chiyani muyenera . . .

    • • kumalankhulana ndi akulu tsoka lisanachitike, likamachitika, komanso pambuyo poti lachitika?

    • • kukhala ndi zinthu zomwe mungazigwiritse ntchito pakachitika ngozi zogwa mwadzidzidzi?​—g17.5 6

    • • kukambirana mitundu ya masoka omwe angachitike komanso zimene mungachite masokawo akachitika?

  • Njira zomwe tingathandizire ena pakachitika ngozi. Chithunzi choyamba: M’bale akupemphera. Chachiwiri: Anthu ongodzipereka akugwira nawo ntchito yopereka thandizo kwa anthu okhudzidwa. Chachitatu: M’bale akuponya ndalama m’bokosi loponyamo zopereka m’Nyumba ya Ufumu.

    Kodi ndi zinthu zitatu ziti zimene tingachite pothandiza anthu omwe akhudzidwa ndi tsoka linalake?

KODI INUYO MUNGADZIPEREKE?

Ntchito yothandiza anthu pakachitika ngozi zogwa mwadzidzidzi ikufunika anthu ambiri. Ngati mukufuna kudzagwira nawo ntchitoyi, uzani akulu mwamsanga.

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani