Mawu Oyamba
Kodi munayamba mwaganizapo kuti Mulungu samva mapemphero anu? Ngati zili choncho, dziwani kuti si inu nokha. Anthu ambiri anapemphapo Mulungu kuti awathandize koma mavuto awo sanathe. Nkhani zotsatirazi ziyankha mafunso awa: Kodi n’chifukwa chiyani sitiyenera kukayikira kuti Mulungu amamva mapemphero athu? N’chifukwa chiyani mapemphero ena sayankhidwa? Nanga kodi tiyenera kuchita chiyani kuti mapemphero athu aziyankhidwa?