Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • w23.12 103
  • Zochitika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Zochitika
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kuchitira Chifundo Anthu Onse
  • Tizitsanzira Yehova pa Nkhani ya Chifundo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2017
  • Kodi Mwakonzekera Chisautso Chachikulu?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Tizimvetsera Anthu, Kuwadziwa Komanso Kuwachitira Chifundo
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2020
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
w23.12 103

Zochitika

Kuchitira Chifundo Anthu Onse

Tsiku lina mlongo wina wa ku New Zealand anaonera vidiyo pa jw.org yomwe inkafotokoza kuti Yehova samangomva chifundo mumtima koma amachisonyezanso. (Yes. 63:​7-9) Iye anaganiza zotsatira mfundo za muvidiyoyi pofufuza mpata woti athandize ena.Tsiku lomwelo atapita kukagula zinthu anakumana ndi mayi amene analibe pokhala ndipo anamufunsa ngati angafune kuti amugulire chakudya. Mayiyo anavomera. Mlongoyo atabwera ndi chakudya, anamulalikira mwachidule pogwiritsa ntchito kapepala kakuti, Kodi Mavuto Amene Tikukumana Nawowa Adzathadi?

Mayiyo anangoyamba kulira. Anafotokoza kuti anakulira m’banja la Mboni koma anasiya choonadi zaka zambiri m’mbuyomo. Koma chaposachedwa wakhala akupemphera kwa Yehova kuti amuthandize kubwerera kwa iye. Mlongoyo anamupatsa mayiyo Baibulo n’kukonza zoti aziphunzira naye.a

Mofanana ndi Yehova nafenso tikhoza kuchitira chifundo anthu kuphatikizapo achibale athu komanso abale ndi alongo mumpingo. Tingasonyezenso chifundo pofufuza mipata yoti tilalikire anthu ena.

a Kuti muone mmene mungathandizire anthu amene anafooka, onani nkhani yakuti “Bwererani kwa Ine” mu Nsanja ya Olonda ya June 2020.

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani