Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • w25.3 13
  • Dzanja la Yehova Si Lalifupi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dzanja la Yehova Si Lalifupi
  • Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ZIMENE TINGAPHUNZIRE KWA MOSE NDI AISIRAELI
  • TIKAKUMANA NDI MAVUTO A ZACHUMA
  • KUKONZEKERA ZAM’TSOGOLO
  • Zimene Tikuphunzira pa Mawu Omaliza a Amuna Okhulupirika
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
  • Zosankha Zomwe Zimasonyeza Kuti Timadalira Yehova
    Utumiki Komanso Moyo Wathu Wachikhristu—2023
  • Tizivomereza Modzichepetsa Kuti Sitikudziwa Zonse
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
  • Muzikumbukira Yehova Yemwe ndi “Mulungu Wamoyo”
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2024
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2025
w25.3 13

NKHANI YOPHUNZIRA 13

NYIMBO NA. 4 “Yehova Ndi M’busa Wanga”

Dzanja la Yehova Si Lalifupi

“Kodi dzanja la Yehova ndi lalifupi?”​—NUM. 11:23.

ZIMENE TIPHUNZIRE

Nkhaniyi itithandiza kuti tipitirize kudalira Yehova komanso kuti tisamakayikire kuti angatipatse zimene timafunikira.

1. Kodi Mose anasonyeza bwanji kuti ankadalira Yehova potsogolera Aisiraeli kuchoka ku Iguputo?

BUKU la Aheberi limatchula anthu ambiri amene ankakhulupirira Yehova. Mmodzi wa anthu amenewa ndi Mose. (Aheb. 3:2-5; 11:23-25) Iye anasonyeza chikhulupiriro pamene ankatsogolera Aisiraeli pochoka ku Iguputo ndipo sanaope Farao ndi asilikali ake. Mose anadalira Yehova ndipo anatsogolera Aisiraeli kuwoloka Nyanja Yofiira komanso podutsa m’chipululu. (Aheb. 11:27-29) Aisiraeli ambiri ankakayikira zoti Yehova angawasamalire koma Mose anapitirizabe kudalira Mulungu. Mpake kuti iye ankadalira Mulungu, chifukwa Yehovayo anachita zinthu modabwitsa popereka madzi ndi chakudya kwa anthuwo m’chipululu.a​—Eks. 15:22-25; Sal. 78:23-25.

2. N’chifukwa chiyani Mulungu anafunsa Mose kuti: “Kodi dzanja la Yehova ndi lalifupi?” (Numeri 11:21-23)

2 Ngakhale kuti Mose anali ndi chikhulupiriro cholimba, pa nthawi ina anakayikira zoti Yehova angapereke nyama kwa anthu ake. Patatha pafupifupi chaka kuchokera pamene anatuluka ku Iguputo, Yehova analonjeza anthu ake kuti adzawapatsa nyama. Mose anakayikira ngati Yehova angapereke nyama yokwanira anthu mamiliyoni omwe anali m’chipululu. Poyankha, Yehova anafunsa Mose kuti: “Kodi dzanja la Yehova ndi lalifupi?” (Werengani Numeri 11:21-23.) Mawu akuti “dzanja la Yehova” akuimira mzimu woyera kapena kuti mphamvu imene Mulungu amaigwiritsa ntchito pochita zinthu. Apa tingati Yehova ankafunsa Mose kuti, ‘Kodi ukuganiza kuti sindingathe kuchita zomwe ndikunenazi?’

3. N’chifukwa chiyani tiyenera kuchita chidwi ndi zimene zinachitikira Mose ndi Aisiraeli?

3 Kodi munakayikirapo kuti Yehova adzakupatsani zofunika pa moyo wanu ndi wa banja lanu? Kaya zimenezi zinakuchitikirani kapena ayi, tiyeni tikambirane nkhani ya Mose ndi Aisiraeli omwe ankakayikira zoti Mulungu angawapatse zimene ankafunikira. Mfundo za m’Malemba zomwe tikambirane zitithandiza kuti tizikhulupirira kuti dzanja la Yehova si lalifupi.

ZIMENE TINGAPHUNZIRE KWA MOSE NDI AISIRAELI

4. N’chifukwa chiyani anthu ambiri anayamba kukayikira zoti Yehova angawapatse chakudya?

4 Kodi chinachitika n’chiyani kuti Aisiraeli ambiri ayambe kukayikira zoti Yehova angawapatse zimene ankafunikira? Aisiraeli limodzi ndi “gulu la anthu a mitundu yosiyanasiyana” anakhala m’chipululu kwa kanthawi pa ulendo wawo wochoka ku Iguputo kupita ku Dziko Lolonjezedwa. (Eks. 12:38; Deut. 8:15) Anthu a mitundu yosiyanasiyanawo anayamba kudandaula kuti atopa ndi kudya mana. Aisiraeli nawonso anayamba kudandaula. (Num. 11:4-6) Anthuwo anayamba kulakalaka zakudya zomwe anali nazo ku Iguputo. Mose atapanikizika anayamba kuganiza kuti iyeyo ndi amene amayenera kuwapatsa anthuwo chakudya.​—Num. 11:13, 14.

5-6. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Aisiraeli anatengera kwa anthu ena?

5 N’zoonekeratu kuti Aisiraeli anatengera kusayamikira kwa anthu a mitundu ina. Ifenso tikhoza kutengera mtima wosayamikira umene anthu ali nawo ndipo sitingamasangalale ndi zimene Yehova amatipatsa. Zimenezi zingachitike makamaka pamene tikuganizira zimene tinali nazo kale kapenanso tikamasirira zimene anthu ena ali nazo. Koma kaya zinthu zili bwanji, tikhoza kumasangalala tikakhala ndi mtima woyamikira.

6 Aisiraeli ankafunika kukumbukira kuti Mulungu anawalonjeza kuti adzapeza zinthu zabwino akafika m’Dziko Lolonjezedwa. Lonjezolo linali loti lidzakwaniritsidwa akafika m’dziko latsopano osati m’chipululu. Ifenso tingachite bwino kumaganizira zimene Yehova walonjeza kuti adzatipatsa m’dziko latsopano m’malo momaganizira zinthu zimene tilibe m’dzikoli. Tiziganiziranso malemba amene angatithandize kuti tizikhulupirira kwambiri Yehova.

7. N’chifukwa chiyani tiyenera kukhulupirira kuti dzanja la Yehova si lalifupi?

7 Komabe mwina mungadabwe kuti n’chifukwa chiyani Mulungu anafunsa Mose kuti: “Kodi dzanja la Yehova ndi lalifupi?” Yehova ayenera kuti ankafuna kuthandiza Mose kudziwa zinthu ziwiri. Choyamba, dzanja la Yehova ndi lamphamvu kwambiri. Ndipo chachiwiri, likhoza kufika paliponse pofuna kuthandiza anthu. Mulungu akanatha kuwapatsa Aisiraeli nyama ngakhale kuti anali kuchipululu kwaokha. Choncho Mulungu anagwiritsa ntchito “dzanja lamphamvu komanso mkono wotambasula” kuti awathandize. (Sal. 136:11, 12) Ifenso tikakumana ndi mavuto tisamakayikire kuti dzanja la Yehova likhoza kutipeza n’kutithandiza.​—Sal. 138:6, 7.

8. Kodi tingapewe bwanji zimene anthu ena anachita m’chipululu? (Onaninso chithunzi.)

8 Pasanapite nthawi, Yehova anakwaniritsa zimene analonjeza ndipo anapatsa anthuwo zinziri zambirimbiri. Koma Aisiraeli sanayamikire zinthu zodabwitsa zimene Mulungu anawachitira. M’malomwake ambiri anasonyeza mtima wadyera. Iwo anagwira zinziri zambiri kwa tsiku lonse. Yehova anakwiya ndi anthu “amene anasonyeza mtima wadyera” ndipo anawalanga. (Num. 11:31-34) Kodi tikuphunzirapo chiyani? Tiyenera kusamala kuti tisayambe mtima wadyera. Kaya ndife olemera kapena osauka, tiyenera kuyesetsa kuti tisunge ‘chuma chathu kumwamba’ pokhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova komanso Yesu. (Mat. 6:19, 20; Luka 16:9) Tikatero sitingakayikire ngakhale pang’ono kuti Yehova adzatisamalira.

Aisiraeli akugwira zinziri zambirimbiri usiku m’chipululu.

Kodi anthu ambiri anasonyeza mtima wotani m’chipululu, nanga tikuphunzirapo chiyani? (Onani ndime 8)


9. Pa nkhani yoti Mulungu adzatithandiza, kodi tingakhale otsimikiza za chiyani?

9 Yehova ndi wokonzeka kuthandiza anthu ake masiku ano. Koma zimenezi sizikutanthauza kuti sitingasowe ndalama kapena chakudya. Apa mfundo ndi yakuti Yehova sangatisiye tokha. Iye adzatisamalira pa mavuto osiyanasiyana amene tingakumane nawo. Tiyeni tikambirane mmene tingasonyezere kuti timakhulupirira kuti Yehova adzatisamalira (1) tikakumana ndi mavuto a zachuma, (2) tikamaganizira za mmene tingadzapezere zofunika m’tsogolo.

TIKAKUMANA NDI MAVUTO A ZACHUMA

10. Kodi tingakumane ndi mavuto a zachuma ati?

10 Pamene mapeto a dzikoli akuyandikira, mavuto a zachuma aziwonjezereka. Zinthu monga mavuto a zandale, nkhondo, ngozi za m’chilengedwe kapena miliri, zingayambitse mavuto azachuma. Zingatiwonongere ndalama, katundu, nyumba kapenanso ntchito ingatithere. Tingafunike kusaka ntchito ina kapena kusamukira kudera lina n’cholinga choti tizisamalira banja lathu. Ndiye n’chiyani chingatithandize kuti tizidalira Yehova posankha zochita?

11. Kodi n’chiyani chingakuthandizeni mukakumana ndi mavuto a zachuma? (Luka 12:29-31)

11 Chinthu chofunika kwambiri chomwe mungachite ndi kupemphera kwa Yehova. (Miy. 16:3) Muzimupempha kuti akuthandizeni kusankha bwino zochita komanso kuti akuthandizeni kuti ‘musamavutike mumtima’ chifukwa cha mavuto anu. (Werengani Luka 12:29-31.) Muzimupemphanso kuti akuthandizeni kukhala ndi mtima woyamikira. (1 Tim. 6:7, 8) Muzifufuza m’mabuku athu kuti mudziwe zimene mungachite ngati mwakumana ndi mavuto a zachuma. Anthu ambiri amanena kuti nkhani za pa jw.org zinawathandiza pamene anakumana ndi mavuto a zachuma.

12. Kodi ndi mafunso ati amene angathandize Mkhristu posankha zochita zokhudza banja lake?

12 Anthu ena avomerapo kukagwira ntchito kutali ndi banja lawo koma zotsatira zake sizimakhala zabwino. Mukamasankha ntchito, musamangoganizira ndalama zimene mungapeze. Koma muziganiziranso mmene zingakhudzire ubwenzi wanu ndi Yehova. (Luka 14:28) Mungadzifunse kuti: ‘N’chiyani chingachitikire banja langa ngati nditapita kutali? Kodi ndizikwanitsa kupezeka pamisonkhano komanso mu utumiki?’ Ngati muli ndi ana muyeneranso kudzifunsa funso lofunika ili: ‘Ngati nditachoka, kodi ndingalere bwanji ana anga “powapatsa malangizo komanso kuwaphunzitsa mogwirizana ndi zimene Yehova amanena?”’ (Aef. 6:4) Muziyendera maganizo a Mulungu osati a achibale kapena anzanu amene salemekeza mfundo za m’Malemba.b Tony, yemwe amakhala kumadzulo kwa Asia, wakhala akupemphedwa maulendo angapo kuti akagwire ntchito yabwino kunja. Koma ataipempherera nkhaniyi komanso kukambirana ndi mkazi wake anaganiza zoti asalole. M’malomwake anakambirana zoti achepetse zinthu zimene banja lawo linkagula. Tonny anati: “Pofika pano ndathandiza anthu ambiri kudziwa Yehova ndipo ana athu amakonda choonadi. Banja lathu laphunzira kuti ngati titatsatira lemba la Mateyu 6:33, Yehova adzatisamalira.”

KUKONZEKERA ZAM’TSOGOLO

13. Kodi ndi zinthu ziti zomwe tingachite pokonzekera zam’tsogolo?

13 Kodi tingasonyezenso bwanji kuti timadalira Yehova tikamakonzekera zam’tsogolo pa nthawi imene tidzakhale titakalamba? Baibulo limatilimbikitsa kuti tizigwira ntchito mwakhama kuti tisadzavutike kupeza zofunika pa moyo m’tsogolo. (Miy. 6:6-11) Ngati n’zotheka, ndi nzeru kusunga ndalama inayake kuti tidzagwiritse ntchito m’tsogolo. Ndalama imateteza ndithu. (Mlal. 7:12) Koma tisalole kuti kufuna ndalama kukhale chinthu chofunika kwambiri pa moyo wathu.

14. N’chifukwa chiyani tiyenera kuganizira lemba la Aheberi 13:5 tikamakonzekera zam’tsogolo?

14 Yesu anasonyeza kuti si nzeru kukhala ndi ndalama popanda kukhala “wolemera kwa Mulungu.” (Luka 12:16-21) Pajatu amati zamawa sizidziwika. (Miy. 23:4, 5; Yak. 4:13-15) Akhristufe timakumananso ndi vuto lina. Yesu ananena kuti tiyenera kukhala okonzeka kusiya chuma chathu kuti tikhale ophunzira ake. (Luka 14:33) Akhristu a ku Yudeya analolera kusiya zinthu zawo ndipo sankadandaula. (Aheb. 10:34) Masiku anonso abale ndi alongo ambiri alolera kusiya zinthu zawo kapena ntchito n’cholinga choti asalowerere ndale. (Chiv. 13:16, 17) Kodi n’chiyani chinawathandiza kuchita zimenezo? Iwo amakhulupirira kwambiri lonjezo la Yehova lakuti: “Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.” (Werengani Aheberi 13:5.) Timayesetsa kukonzekera zam’tsogolo, koma tikakumana ndi mavuto amwadzidzidzi timakhulupirira kuti Yehova adzatithandiza.

15. Kodi makolo ayenera kukhala ndi maganizo ati pa nkhani ya ana awo? (Onaninso chithunzi.)

15 M’zikhalidwe zina, mabanja amakhala ndi ana n’cholinga choti anawo adzathandize makolo awowo akadzakalamba. Baibulo limanena kuti makolo ayenera kusamalira ana awo. (2 Akor. 12:14) N’zoona kuti makolo akakalamba amafunika kuthandizidwa ndi ana awo ndipo ana ambiri amasangalala kuchita zimenezi. (1 Tim. 5:4) Koma makolo a Chikhristu amazindikira kuti angakhale osangalala kwambiri ngati atakhala ndi ana, n’kuwathandiza kukhala atumiki a Yehova, osati kukhala nawo n’cholinga choti adzawathandize m’tsogolo.​—3 Yoh. 4.

Banja la Chikhristu likulankhulana ndi mwana wawo pa vidiyokomfelensi. Mwanayo ndi mwamuna wake avala malifulekita ovala pa ntchito zomangamanga.

Akhristu okhulupirika amatsatira mfundo za m’Baibulo akamaganizira zam’tsogolo. Zimenezi zikuphatikizapo kuchuluka kwa ana amene angakhale nawo (Onani ndime 15)c


16. Kodi makolo angatani pokonzekeretsa ana awo kuti azidzapeza zofunika pa moyo? (Aefeso 4:28)

16 Muziwapatsa ana anu chitsanzo pa nkhani yodalira Yehova. Muziwaphunzitsa kugwira ntchito mwakhama kuyambira ali aang’ono. (Miy. 29:21; werengani Aefeso 4:28.) Akamakula muziwauza kuti azilimbikira kusukulu. Makolo ayenera kufufuza komanso kugwiritsa ntchito mfundo za m’Baibulo pothandiza ana awo kuti azigwiritsa ntchito bwino maphunziro. Izi zingadzawathandize kuti azidzapeza zofunika pa moyo uku akutumikira Yehova.

17. Kodi sitiyenera kukayikira za chiyani?

17 Atumiki a Yehovafe tiyenera kumudalira kuti ali ndi mphamvu komanso mtima wofunitsitsa kutithandiza kupeza zofunika. Pamene mapeto a dzikoli akuyandikira, tidzayesedwa pa nkhani yodalira Yehova. Ndiye kaya tikumana ndi zotani, tiyenera kumadalira kuti Yehova adzagwiritsa ntchito mphamvu zake potithandiza kupeza zofunika pa moyo. Tisamakayikire kuti mkono wake wotambasula komanso dzanja lake lamphamvu likhoza kutithandiza kulikonse kumene tili.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhani ya Mose ndi Aisiraeli?

  • Kodi tingasonyeze bwanji kuti timadalira Yehova tikakumana ndi mavuto a zachuma?

  • Kodi tiyenera kuganizira chiyani tikamakonzekera zam’tsogolo?

NYIMBO NA. 150 Bwerani kwa Mulungu Kuti Mupulumuke

a Onani “Mafunso Ochokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya October 2023.

b Onani nkhani yakuti “Simungatumikire Ambuye Awiri” mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 2014.

c MAWU OFOTOKOZERA CHITHUNZI: Banja la Chikhristu likulankhulana ndi mwana wawo yemwe akutumikira ndi mwamuna wake pantchito yomanga Nyumba ya Ufumu.

    Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
    • tumizirani
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • zachinsinsi
    • JW.ORG
    • Lowani
    tumizirani