Mawu a M'munsi
b Zimenezi zingamveke ngati zodabwitsa, koma sizinali zachilendo m’nthawi imeneyo. Mwachitsanzo, katswiri wina wachigiriki wolemba mbiri yakale, dzina lake Herodotus, anafotokoza kuti pa nthawi ina Aperisi analira maliro a kazembe winawake wotchuka, ndipo anachita mwambo wa malirowo limodzi ndi ziweto zawo zomwe.