Mawu a M'munsi
b MATANTHAUZO A MAWU ENA: Kukhulupirira mizimu kumatanthauza kukhulupirira kapena kuchita zinthu zokhudzana ndi ziwanda. Anthu okhulupirira mizimu amakhulupirira kuti munthu akafa mzimu wake umakhalabe ndi moyo ndipo tikhoza kulankhula naye kudzera mwa anthu ena. Amathanso kuchita zinthu zodabwitsa, zamatsenga komanso zokhudza ufiti. Ena amati akhoza kutemberera munthu, kulodza kapena kuchesula.