Mawu a M'munsi
b TANTHAUZO LA MAWU ENA: Kudzozedwa ndi mzimu woyera: Yehova amagwiritsa ntchito mzimu wake woyera kusankha munthu kuti akalamulire ndi Yesu kumwamba. Pogwiritsa ntchito mzimu wake, Mulungu amapatsa munthuyo “chikole” kapena kuti kumulonjeza zinthu zam’tsogolo. (Aef. 1:13, 14) Akhristu amenewa anganene kuti mzimu woyera “umachitira umboni,” kapena kuti kuwatsimikizira kuti mphoto yawo ili kumwamba.—Aroma 8:16.