Mawu a M'munsi
b Buku lina linanena kuti, “m’Baibulo la Chipangano Chatsopano mulibe lemba losonyeza kuti makanda ayenera kubatizidwa.” Bukuli linanenanso kuti ubatizo wa makanda unachokera pa “maganizo olakwika komanso ongokokomeza omwe anthu anali nawo pa nkhani ya kufunika kwa ubatizo.” (The International Standard Bible Encyclopedia, Volume 1, page 416-417) Anthuwo anali ndi maganizo akuti ubatizo paokha umachotseratu machimo a munthu.