Kodi Baibulo Lingandithandize Kupirira Matenda?
Yankho la m’Baibulo
Inde. Mulungu amaganizira atumiki ake amene akudwala. Ponena za mtumiki wa Mulungu wokhulupirika, Baibulo limati: ‘Yehova adzamuchirikiza pamene akudwala pabedi lake.’ (Salimo 41:3) Ngati mukudwala matenda enaake, mfundo zitatu zotsatirazi zingakuthandizeni kupirira.
- Muzipempha Mulungu kuti akupatseni mphamvu. Mulungu angakupatseni ‘mtendere wake umene umaposa kuganiza mozama kulikonse,’ womwe ungakuthandizeni kuti mupirire komanso kuti musamade nkhawa kwambiri.—Afilipi 4:6, 7. 
- Muziyesetsa kukhala wosangalala. Baibulo limati: “Mtima wosangalala ndiwo mankhwala ochiritsa, koma mtima wosweka umaumitsa mafupa.” (Miyambo 17:22) Muziyesetsa kuseka kapena kuchita tinthabwala chifukwa zimenezi zimathandiza kuti muziiwalako mavuto. Izi zingathandizenso kuti musamavutike kwambiri ndi matendawo. 
- Muzikhulupirira zimene Mulungu walonjeza. Mukamayembekezera zinthu zabwino mukhoza kukhala osangalala ngakhale kuti mukuvutika ndi matenda. (Aroma 12:12) Baibulo limatiuza kuti m’tsogolomu, palibe munthu amene “adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’” (Yesaya 33:24) Pa nthawiyo, Mulungu adzathetsa matenda onse, ngakhale amene anthu akulephera kuwachiza masiku ano. Mwachitsanzo, Baibulo limanena zimene Mulungu adzachite pothetsa ukalamba. Limati: “Mnofu wake usalale kuposa mmene unalili ali mnyamata. Abwerere ku masiku ake aunyamata pamene anali ndi mphamvu.”—Yobu 33:25. 
Dziwani izi: A Mboni za Yehova amadziwa kuti Mulungu amathandiza anthu amene akudwala koma nawonso amalandira chithandizo chamankhwala akadwala. (Maliko 2:17) Sitilimbikitsa anthu kulandira chithandizo chinachake chifukwa munthu aliyense ayenera kusankha yekha chithandizo chimene akufuna.