NYIMBO 135
Yehova Akutipempha Kuti: “Mwana Wanga, Khala Wanzeru”
zosindikizidwa
1. Mwana wanga undipatse
mtima wako.
Yemwe akunditonza
aone yekha.
Ukudziperekadi
mofunitsitsa;
Anthu adziwe
kuti umandikonda.
(KOLASI)
Mwana wanga wokondedwawe,
Khalatu wanzeru chonde.
Kutitu unditumikire,
Inde mwakufuna kwako.
2. Uzinditumikira
mosangalala,
Ngakhale ukapunthwa,
ndidzakudzutsa.
Wina ngakhale
angakukhumudwitse,
Usadere nkhawa
ndidzakhala nawe.
(KOLASI)
Mwana wanga wokondedwawe,
Khalatu wanzeru chonde.
Kutitu unditumikire,
Inde mwakufuna kwako.
(Onaninso Deut. 6:5; Mlal. 11:9; Yes. 41:13.)