NYIMBO 83
“Kunyumba ndi Nyumba”
zosindikizidwa
1. Ife timalalikira
Kunyumba ndi nyumba.
Kulikonse nkhosa za M’lungu
Zikudyetsedwa.
Tonse, akulu ndi ana,
Tikulalikira
Zoti Ufumu wa M’lungu
Ukulamulira.
2. Khomo ndi khomo,
Tinene za chipulumutso.
Aitane dzina la M’lungu
Apulumuke.
Angaitane bwanji
Dzina sakulidziwa?
Choncho kunyumba zawo
Tikawalalikire.
3. Khomo ndi khomo,
Tiyeni tikalalikire.
Asankhe okha kumvera
Kapena kukana.
Koma dzina la Yehova
Tidzalengezabe.
Tikamatero,
Tidzapezadi nkhosa zake.
(Onaninso Mac. 2:21; Aroma 10:14.)