NYIMBO 52
Kudzipereka Monga Mkhristu
zosindikizidwa
1. Yehova Mulungu wathu
Analenga zonse.
Dzikoli ndi mlengalenga
Zonsezi ndi zake.
Iye watipatsa moyo,
Wasonyeza kuti
Ndi woyenera kum’tamanda
Ndiponso kum’lambira.
2. Yesu atabatizidwa
Anauza M’lungu:
‘Ndabwera kuti ndichite
Chifuniro chanu.’
Mulungu anamudzoza
Atabatizidwa
Kuti azimutumikira
Monga wodzipereka.
3. Yehova ife tabwera
Kukutamandani.
Tadzipereka kwa inu
Ndipo tadzikana.
Munatikonda kwambiri
Potipatsa Yesu.
Tasiya zomwe timafuna
Tizichita za inu.
(Onaninso Mat 16:24; Maliko 8:34; Luka 9:23.)