NYIMBO 142
Tigwire Mwamphamvu Chiyembekezo Chathu
zosindikizidwa
1. Anthu akhala akuyenda mumdima.
Ndipo sanapindule kalikonse.
Zadziwika kuti anthu ochimwa;
Kuvutika sangakuthetse.
(KOLASI)
Tiyeni tiimbe mokondwera!
Poti Ufumu wa M’lungu wabwera.
Yesu adzachotsadi zoipa;
Chiyembekezochi n’chodalirika.
2. Uthenga womwe ukumveka ndi woti;
“Tsiku la Mulungu layandikira.”
Anthu sadzakhalanso ndi chisoni.
M’lungu wathu timuimbira.
(KOLASI)
Tiyeni tiimbe mokondwera!
Poti Ufumu wa M’lungu wabwera.
Yesu adzachotsadi zoipa;
Chiyembekezochi n’chodalirika.
(Onaninso Sal. 27:14; Mlal. 1:14; Yow. 2:1; Hab. 1:2, 3; Aroma 8:22.)