NYIMBO 129
Tipitirizebe Kupirira
zosindikizidwa
	- 1. Tizipirira - Mayesero ngati Yesu. - Anavutika - Koma ankasangalala - Ndi chiyembekezo. - Analimba mtima. - (KOLASI) - Tikhale opirira. - Tizilalikira. - M’lungu amatikonda - Adzatithandiza kupirira. 
- 2. Tingakumane - Ndi mavuto ochuluka, - Tidikirebe - Moyo wosatha m’tsogolo. - Tikulakalaka - Mtendere wosatha. - (KOLASI) - Tikhale opirira. - Tizilalikira. - M’lungu amatikonda - Adzatithandiza kupirira. 
- 3. Sitimaopa - Kapena kukayikira. - Titumikire - Mpaka tsiku lomaliza. - Tsiku la Yehova - Lilidi pafupi. - (KOLASI) - Tikhale opirira. - Tizilalikira. - M’lungu amatikonda - Adzatithandiza kupirira. 
(Onaninso Mac. 20:19, 20; Yak. 1:12; 1 Pet. 4:12-14.)