NYIMBO 94
Timayamikira Mulungu Potipatsa Mawu Ake
zosindikizidwa
	- 1. Yehova Atate, tikuthokoza - Chifukwa Mawu anu mwatipatsa. - Munawauziradi; - Anatimasula. - Kuwala kwake kwatipatsa nzeru. 
- 2. Mawu anu ndi amphamvu kwambiri. - Maganizo n’zolinga ’lekanitsa. - Ndiponso malamulo, - Anu n’ngolungama. - Mfundo zanu zimatitsogolera. 
- 3. Mawu anu M’lungu, amatikhudza. - Aneneri anu anali anthu, - Chonde tithandizeni - Tikhulupirire. - Mwatipatsa Mawu, tathokoza Ya. 
(Onaninso Sal. 19:9; 119:16, 162; 2 Tim. 3:16; Yak. 5:17; 2 Pet. 1:21.)