NYIMBO 96
Baibulo Ndi Chuma
zosindikizidwa
	- 1. Pali buku limene mawu ake - Amatibweretsera chimwemwe. - Mfundo zake zodabwitsa n’zamphamvu, - Limapatsa nzeru owerenga. - Bukuli ndi Baibulo loyera. - Olilemba anauziridwa. - Ankakonda Yehova M’lungu wawo, - Mzimu wake unawathandiza. 
- 2. Analemba zokhudza chilengedwe, - Mmene M’lungu anachilengera. - Analembanso za Paradaiso - Ndiponso za mmene anathera. - Analemba za mngelo winawake - Amene ananyoza Yehova. - Anabweretsa mavuto pa anthu - Koma Yehova adzapambana. 
- 3. Masiku ano tikusangalala - Ufumu wa Mulungu wayamba. - Tiuze anthu uthenga wabwino - Ndi madalitso omwe abwere. - M’Baibulo muli zosangalatsa. - Chakudya chochuluka kwambiri. - Limatipatsa mtendere wambiri, - Tiyesetse kumaliwerenga. 
(Onaninso 2 Tim. 3:16; 2 Pet. 1:21.)